Zomwe achita a Msonda zaonetsa kukhwima nzeru pandale, watero katakwe pandale


Ken Msonda, a DPP Confusionist, is Controversial

M’modzi mwa akatakwe omwe amatsatira bwino pa nkhani za ndale mdziko lino a Lydford Chadza ayamikira zomwe  achita a Ken Msonda popepesa kwa mtsogoleri wa chipani  cha DPP a Peter Mutharika ndipo iwo ati izi zaonetsa kukhwima mzeru pandale.

A Chadza anafotokoza kuti mpungwepungwe ndi kusamvana komwe kunabuka sikukanatengera kwina kulikonse chipanichi. Kotero iwo apempha kuti omwe anali mbali imodzi ndi a Msonda nawonso achita chimodzimodzi pofuna kumanga chipani.

Angakhale kuti a Msonda amadzetsa mpungwepungwe mchipanichi, koma iwo amadziwa bwino lomwe malamulo oyendetsera chipanichi kuti chimamulora mtsogoleli wakaleyu kuyimira katatu.

A Mutharika anayitanitsa msonkhano wa NSG ku Mangochi, komwe iwo anadzudzula a Msonda pa zomwe akhala akuchita ndipo analamula a Msonda kuti atha kubwerela kuchipani chawo cha kale cha PP.

Wolemba: Ben Bongololo