Azanyengo ati kugwa mvula ya mphamvu kuyambira lachitatu likudzali

Advertisement
Heavy rains are expected to hit Malaiw

Pamene madera amchigawo chapakati komanso kumwera kwa dziko lino kuli nga’mba, tsopano nthambi yoona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo yati kuyambira lachitatu pa 13 December,  a Malawi  ayembekezere kulandira mvula ya mphamvu.

Malingana ndi chikalata chomwe nthambiyi yatulutsa kudzera mwa m’neneri wa nthambiyi a Yobu Kachiwanda ati mvula ikuyembekezereka kugwa mmadera ochuluka mdziko lino.

Iwo ati izi zili chonchi kamba ka nkumano wa mphepo yozizira komanso ya chinyontho yochokera mchigawo chakum’mwera komanso  yotentha kuchokera ku mpoto yomwe iwo akumayitchula kuti ITCZ.

Masiku apitawo mvula yamphamvuyi yaonongapo zinthu zosiyanasiyana m’madera monga a Salima ndi ena Kotero a Malawi akuyenera kukhala osamala mmaka nyengo imeneyi.

Advertisement