Nankhumwa wati ndege ya ku Israel ikuzatenga achinyamata 221 ku Malawi


Kondwani Nankhumwa Malawi

Mtsogoleri wa mbali yotsutsa mu Nyumba ya Malamulo, a Kondwani Nankhumwa, wati m’dziko muno mukuyembekezeka kufika ndege kuchokera m’dziko la Israel kuzatenga achinyamata 221 kuti akagwire ntchito mu dziko la Israel.

Nankhumwa wapempha  unduna wa za ntchito kuti ufotokoze chilungamo chenicheni pa za ntchito yomwe achinyamata akukagwira mu dziko la  Israel.

Malingana ndi a Nankhumwa, pali mphekesera kuti achinyamatawa akukamenya nkhondo ya dziko la Israel ndi dziko la Palestine.

A Nankhumwa anenaso kuti achinyamatawa akuyembekezeka kunyamuka m’dziko muno kupita Ku Israel mawa.

Atalakhula a Nankhumwa zokhudza kubwera kwa ndegeyi m’dziko muno, mu Nyumbayi munali mpungwepungwe pomwe a mbali yaboma amafuna kuti mtsogoleri wa mbali yotsutsayi achotse mawu oti dziko la Malawi likufuna kutumiza achinyamata Ku dziko la Israel kuti akamenye nkhondo.

Pakuyankha kwawo, a nduna owona za maubale lino ndi mayiko ena, Nancy Tembo, atsutsa zomwe anakamba a Nankhumwa ndipo akuti ndi zabodza.

Sipikala wa nyumbayi a Catherine Gotani Hara walamula a Nankhumwa kuti abweletse umboni sabata la mawa lolemba.