Ndichitonzo kukweza malipiro ndi K10 pa K100 iliyonse, watero Kalindo


Bon Kalindo (L) is a Malawian activist who has been leading protests during the Lazarus Chakwera admnistration

A Bon Kalindo omwe amachititsa zionetsero lero mu mzinda wa Blantyre apempha boma kuti likweze malipiro a anthu ogwira ntchito m’boma ndi K50 pa K100 iliyonse.

A Kalindo, ati ndichitonzo  kukweza malipiro a ogwira ntchito m’boma ndi 10 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse kutengera kuti ndalama yadziko lino inagwa ndi 44 pelesenti.

Iwo amayankhula izi mu mzinda wa Blantyre komwe amakasiya kalata yofuna kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera athane ndi mavuto omwe akuta dziko lino pasanathe masiku makumi awili.

A Kalindo anaonjezera kuti akumenyeranso ufulu wa apolisi m’dziko muno poti malipiro ndi zovala zawo ndizosalongosoka.

“Kuonanso malipiro apamwezi ndizosalongosoka. Ichi ndichizindikiro choti zinthu sizili bwino,” anatero Kalindo.

A Kalindo ati akufunanso kuti a Chakwera komanso  wachiwiri wawo a Saulos Chilima atule pansi ma udindo awo.

Kulephera kwa boma kulemba ntchito achinyamata, kugwa mphamvu ya kwacha komanso nkhani yokhudza ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya AIP ndi enanso mwa madandaulo omwe akuchitira zionetserozi.

A Charles Mphepo omwe ndi ogwira ntchito ku Khonsolo ya mzinda wa Blantyre ndi omwe analandira kalata ya madandauloyi kuchokera kwa a Kalindo omwe  akufuna kuti ikaperekedwe kwa mtsogoleri wa dziko lino.