ACB yakhazikitsa bukhu

Advertisement
ACB and Ministry of Education have released a book for primary schools

Bungwe lothana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau lakhazikitsa bukhu la tsopano lotchedwa “Anti-Corruption Source Book” lomwe lidzigwilisidwa ntchito ndi aphunzitsi a kupulaimale.

Bukhuli lomwe alikhazikitsa dzulo ku Lilongwe cholinga chake ndi kuphunzitsa chikhalidwe, umunthu komanso mzimu wa kulimbikira pakati pa ana m’dziko muno.

Oyang’anila ntchito ku bungweli a Martha Chizuma, anati, bukhuli lithandiza kubwelesa m’bado watsopano opanda chinyengo.

Mu mau ake, mlembi ku unduna wa maphunziro a Chikondano Mussa, anati, undunawu ukuunikaso maphunziro a dziko lino ndipo kuti ma uthenga okhudza kuthana ndi katangale azaikidwa m’maphunziro ena.

Bukhuli Anti-Corruption Source Book lakhadzikitsidwa pa mutu oti Maphunziro Umunthu ndi cholinga chothana ndi katangale.

Olemba Andrew Salima

Advertisement