Sing’anga alipilitsidwa chindapusa atakanika kudzutsa munthu omwalira

Advertisement
court

Bwalo loweluza milandu m’boma la Balaka lalamula kuti bambo wina wa zaka 37 zakubadwa, a Frazer Satha omwe ndi sing’anga wa zitsamba, alipile chindapusa cha ndalama zokwana K90,000 apo bii akagwire ntchito ya kalavulagaga ku ndende kwa miyezi khumi ndi isanu (15) atawapeza olakwa pa mlandu opeza ndalama mwa chinyengo.

Oyimira boma pa milandu a sub-Inspector Mercy Chande adauza bwalo la milandu kuti mu mwezi wa June chaka chino, mkuluyu adanamiza a Yamikani Tobias omwe amakhala mu dera la Andiamo m’bomali kuti iwo ali ndi kuthekera kodzutsa mwana wawo yemwe panthawi yomwe amkamwalira mu mwezi wa August chaka chatha adali ali ndi zaka 18 zakubadwa.

A chande adati a Tobias atamva izi sadazengeleze koma kulipira ndalama yokwana K45,000 kwa ng’angayu ndi chiyembekezo chakuti mwana wawo awuka ku imfa zomwe sizidachitike konse.

Izitu akuti zidawapangitsa odandaulawa kukamang’ala ku Police, zomwe zidapangitsa kuti ng’angayi ayitsekele mu chitokosi cha Police.

Koma itawonekera mu bwalo la milandu, ng’angayi idakana kuvomera mlandu opeza ndalama mwachinyengo zomwe ndi zosemphana ndi gawo 319 la malamulo a dziko lino. Izi zidapangitsa bwalo la milandu kuti liyitanitse mboni zitatu ndipo pamapeto pake ng’angayi adaipeza yolakwa pa mlanduwu.

Ndipo oyankha mlanduwu adapempha bwalo kuti limupatse chilango chofewa kunena kuti iye ali ndi banja lomwe amalisamalira. Komabe, oyimira boma pa mlanduwu, a Mercy Chande adapempha bwaloli kuti lipeleke chilango chokhwima kuti ena atengelepo phunziro.

Oweruza mlandu a Lucy Mukawa adavomerezana ndi zomwe a Chande adanena ndipo adalamula kuti ng’angayi ilipira chi ndapusa cha ndalama zokwana K90,000 ndipo ikalephera kupeleka ndalamayi ikagwire ntchito ya kalavulagaga kwa miyezi khumi ndi isanu (15).

Pakadali pano, a Satha omwe amachokera m’mudzi wa Madzanje, mfumu yaikulu Kwataine m’bola la Ntcheu apeleka kale chindapusachi.

Advertisement