Sindinati, ndisiya pokhapokha kayendetsedwe ka mpira kasinthe, watelo De Jongh


Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers Pieter De Jongh yemwe akuoneka kuti alibe zoti kuno mkuchilendo wati ngati akuluakulu sasintha kayendetsedwe ka mpira wa miyendo mdziko muno, iye apitilirabe kudzudzula pazolakwika zonse zomwe akuziona.

De Jongh yemwe anafika mdziko muno kumayambiliro kwa chaka chino kudzaphuzitsa timu ya Silver Strikers wati zinthu zambiri ndizofunika zitasinthidwa m’masewero a mpira wa miyendo mdziko muno.

Iye wadzudzula zomwe zinachitika lamulungu pa bwalo la Chiwembe pomwe akuluakulu a matimu a Mighty Tigers komanso Mighty Mukuru Wanderers anasinthana zichewa komaso kugendana ndi zinthu pomwe ma timu awo amakumana.

Iye wati anali odabwa kuti ngakhale kumasewelowa kunali chifwilimbwiti cha ndiwe yani, palibe yemwe inaonesedwa chikalata chofiira (red card).

Iye wati anali odabwa polingalira kuti iye akangochita mphulupulu pang’ono amapatsidwa chilango ndi oyimbira zomwe akuti ukuku sizinachitike.

Iye wati akuona ngati zilango zomwe akumalandira ndizofuna kumutseka pakamwa kuti asamadzudzule zolakwika zomwe akuziona koma wanenetsa kuti wati iye sasiya kudzudzulako.

“Sindingatseke pakamwa nkumaonelera zolakwika, osatheka, izizi ndipitiliza kupanga pokhapokha zitakonzedwa ndi anthu oyendetsa masewerowa.

“Tangoganizani pamasewero omwe analipo kuchiwembe pakati pa Tigers komanso Wanderers kunali kuponyerana zibakera koma palibe yemwe walandira chilango, ineyo kungofunsa zanthawi yoonjezera akuti ndalakwa,” watelo De Jongh.

Iye anaonjezera kuti zilango zomwe akupatsidwa pano ndi kaamba koti anthu sakudziwa kuti iye ndi munthu wabwino kwambiri.

“Ineyo ndimunthu wabwino koma anthu samandivetsetsa ndiye chifukwa chake Pofika padakali pano angondipatsa zilango pazinthu zomwe sindingasekelere kuyang’anira pamene zikulakwika,” waonjezera choncho De Jongh.

Mphunzitsiyu posachedwapa anadzudzulaso akuluakulu oyendetsa mpira kaamba kosasamalira bwalo la zamasewero la Mzuzu lomwe akuti ndiloipa kwambiri ngati bala la wamisala.

De Jongh mwathamo anati ngakhale galu wake yemwe akuti ndi wa zaka zinayi, sangasewere mpira pa bwalo la zamasewero la Mzuzu, ponena kuti galuyo atha kukanitsitsa kaamba kakuonongeka kwa bwaloli.

Follow us on Twitter: