‘Ana anjoka inu’, Dorothy Shonga watopela omwe akumunyogodola za Zeze

Advertisement

M’modzi mwa anthu omwe ali mkamwa mkamwa pano Dorothy Shonga, wasambwadza anthu onse omwe akuti akumamunyogodola zokhudza ubwezi wake ndi oyimba Zeze Kingston, ndipo waulura atsikana ambiri ali ndi zibwezi zochuluka.

Nkhaniyi ikutsatira kubwera poyera kwa Shonga yemwe posachedwapa wadzidzimutsa anthu ochuluka podziwitsa dziko kuti ali m’chikondi ndi oyimba Zeze Kingston.

Chigwereni m’chikondi ndi oyimbayu, Shonga wati akunyogodoledwa ndi anthu ochuluka ndipo pano zafika pomutopetsa zomwe zapangitsa kuti ang’alure onse omwe akumamupatsa malangizowo.

Shonga analemba patsamba lake la Facebook pomwe wadandaula kuti iye akunyogodoledwa kaamba kowulura za ubwezi wake ndi Zeze pomwe anthu ena amabisa okondedwa awo ngati malonda a mphaka.

Iye wati atsikana ochuluka omwe akumunyoza zokhudza ubwezi wake ndi Zeze,ambiri ndiwoti ali ndi zibwezi zoposera chimodzi zomwe zimawapangitsa kuti atsikanawa azikanika kubwera poyera ndi kulengeza za ubwezi wawo.

“Ndiye pali ena oti anazolowela kuyenda ndi anthu oti anaona kamuzu akati andilangize za ZEZE ngati angelo. Mukati muwunjike njonda mwayenda nazo ngati mulu wautaka.

“Pomwe iwo they fail to post their mates cz of (amalephera kuonetsa zibwezi zawo chifukwa cha…) uuuuhhhhhuuuuuule ali ndi azimuna 4. Kubisa wachikondi ngati thumba lachamba,” watelo Shonga.

Shonga wadzudzulaso azimayi omwe akumamuseka ndikumunyogodola kuti ali ndi ana atatu ponena kuti ambiri omwe akumamusekawo bwezi ali ndi ana ochuluka kuposa iye anakapanda kuchotsa pakati.

Iye wati amapanga chibwezi ndi munthu mmodzi pa nthawi imodzi kusiyana ndi zomwe njole zambiri zikupanga zomwe wati zimakhala ndi zibwezi zochuluka ngati mchenga.

“Akati andiveke zaka 49 cz of my kids pomwe iwowo anapanga zima abortion zoposa ana atatuwo. Ana anjoka inu. achule, Abwantasa. Ine I date one man at a time for love not for money or fame and give him my all. Posting him is my preference,” anaonjezera choncho Shonga.

Pakadali pano Shonga wafufuta zomwe analemba pa tsamba lake la mchezo.

Follow us on Twitter:

Advertisement