SRWB yayamba kumanga fakitale yopanga madzi a mumabotolo

Advertisement

Bungwe lomwe limawona zamadzi mchigawo chakum’mwera la Southern Region Water Board layamba ntchito yomanga fakitale yopanga madzi a mumabotolo ndipo ntchitoyi idya ndalama zoposa K2.1 billion.

Poyankhula kwa atolankhani pa Old Naisi Turn Off mu Mdzinda wa Zomba pamalo omwe akumangapo fakitae yopanga madziyo, Infrastructure Development Manager wa Bungwe la SRWB, Engineer Emmanuel Chirwa wati fakitaleyi ayimanga kwa miyezi isanu ndi umodzi (6) ndipo pokutha kwa chaka chino madzi awo adzakhala atafika kale pa msika.

Engineer Chirwa wati iwo adaganiza zopanga madzi ogulitsa a mumabotolo pofuna kuti adzipeza ndalama zothandidzira anthu pankhani ya madzi M’malawi muno ndipo adati madziwa adzidzapezeka mulingo wa 500 ml, 1 litre, 500 litres ndima 20 litres kuti anthu azidzakwanitsa kugula ndipo adzakhala pamtengo wabwino.

Pamenepa iwo ati ntchitoyi ikadzatha idzathandizanso anthu ambiri kuti adzapeze ntchito yokhazikika ndipo idzakwaniritsa njira imodzi ya Boma yothetsa umphawi pakati pa achinyamata

“Chomwe chatilimbitsa mtima ife a SRWB ndichoti tili ndi luso pankhani ya madzi ndipo adzakhala abwino kwambiri komanso otsika mtengo mosakayika konse anthu adzawakonda,” adatero Engineer Emmanuel Chirwa.

Follow us on Twitter:

Advertisement