Zayambika ku manoma: alepherana ndi Tigers

Advertisement

Mwayidziwa bwino nyimbo ya mwana ndi mwana imene amakonda kuimba ma Palestina? Kukhala ngati mwana wake amanena achabale awo a Mighty Mukuru Wanderers kapena kuti Manoma. Zawaonekera lero atalepherana ndi timu ya Mighty Tigers.

Atayamba bwino ligi popambana masewero awo atatu kuti akhale pamwamba kwa sabata zitatu, nyerere lero zakumbutsidwa kuti ligi si zibwana.

Pa masewero amene anachitikira pa bwalo la Mpira, ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre, nyerere zinaoneka kuti zinagwedezedwa lero pamene zinavutika kuti zipeze chigoli.

Mu chigawo choyamba, zinatheramo ndithu nyerere osaona pagolo. Komanso nawo anzawo a Tigers anakanika kuti apaone. Kungokhala ngati anakumana okhaokha.

Atakapumira, mphunzitsi wa chingerezi wa timu ya nyerere a Mark Harrison akuoneka kuti anauza Chichewa anyamata ake, kuwakumbutsa kuti akapunthwa ndiye kuti chikwama atola aneba awo a Bullets.

Nkutheka chinali Chichewa chimenecho chimene chinagwedeza manoma moti anayamba kupanikiza. Mphoto ya kufinya adani awo inapezeka mu mphindi ya chi 61 pamene Mnyamata Gaddie Chirwa wa nyerere anagwetsedwa mu bokosi la penate.

Oyimbila analoza pamalo a ngozi ndipo anali Stanley Sanudi amene anaonetsetsa kuti gulu la nyerere likhale ndi chikhulipiliro. Koma chimwemwe chake chinali chosakhalitsa chifukwa nawo a Tigers anapeza mwayi wawo wa penalty.

Panali patangodutsa mphindi zisanu zenizeni a noma chimwetsereni pamene a Tigers anabwenza ndi kupangitsa kuti masewero akhale 1 kwa 1.

Nyerere zinayesera kuzembera umu ndi umo, koma tsogolo silinaoneke kwenikweni. Zinakankha umu ndi umu koma palibe icho anaphula.

Pamapeto pa masewero, Wanderers 1 ndipo Tigers 1. Ulendo otolera ma pointi onse atatu pa masewera a mu ligi wathera pamenepa.

Padakali pano, nyerere ndi maule afanana ma pointi koma potengera zigoli, maule ndiwo akhala pa mwamba. Kwinaku nayo timu ya Siliva imene kochi wake lero anapatsidwa red card ikuthamangitsa akamuna awiriwa nayo ndi ma pointi ofanana nawo.

Follow us on Twitter:

Advertisement