Gulu la Dzuka Malawi likufuna Atupele akhalenso mtsogoleri wa UDF

Advertisement

Pomwe pangotsala chaka chimodzi kuti Chipani cha United Democratic Front (UDF) chichititse msonkhano wake waukulu osankha komiti yatsopano yoyendetsa chipanichi, gulu lina lomwe likudzitchula kuti Dzuka Malawi labwera poyera kufuna kuti Atupele Muluzi akhale mtsogoleri wachipanichi.

Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani ku Gymkhana Club mu mzinda wa Zomba, Msungichuma wamkulu wagulu la Dzuka Malawi Isaac Austin Lalama wati cholinga cha gulu lawo likufuna kuti Atupele Muluzi akapikisane nawo pampando wa President ku nsonkhano waukulu wachipani omwe udzachitike chaka cha 2023 pofuna kuti adzapikitsane nawo pachisankho cha 2025.

Lalama yemwe adatsogolera msonkhano wa atolankhaniwo adati ngati Atupele Muluzi atakamusankhe ku msonkhano waukuluwo mosakayika konse kuti adzathanso kudzapambana pachisankho chosankha mtsogoleri wadziko la Malawi chaka cha 2025.

Pankhani ya 50+1, Lalama adati ngati chipani cha UDF chingadzapange mgwirizano ndi chipani china pachisankho adzawonetsetsa kuti Atupele Muluzi adzakhale wotsogolera mgwirizanowo ngati President.

Pamenepa iye wapempha Atupele Muluzi kuti akapikasane nawo pampando wautsogoleri wachipani cha UDF chaka cha mawa pamsonkhano wake waukulu wachipanichi.

Gulu la Dzuka Malawi lapempha anthu otsatira Chipani cha UDF kuti amange umodzi ndipo pasakhale kugawikana kulikonse kuti chipanichi chidzathe kudzapambana pachisankho chomwe chidzachitike mdziko muno chaka cha 2025 motsogodzedwa ndi Atupele Muluzi.

“Tikudziwa kuti Atupele Muluzi adasiyila utsogoleri wachipani kwa Mai Lillian Patel koma tiwapemphe kuti abwelerenso kudzatenga udindo wao chifukwa zikuwoneka kuti Chipani cha UDF chikulowa pansi,” adatero Isaac Austin Lalama.

Pakali pano gulu la Dzuka Malawi lili ndi mamembala 1,345 ndipo cholinga chake ndikufuna kukakamiza Atupele Muluzi kuti abwelerenso kukhala mtsogoleri wachipani cha UDF.

Follow us on Twitter:

Advertisement