M’busa ‘wadya’ nkhosa, mwini nkhosa wanyangala

Advertisement
Malawi24.com

Kulibe kupuma ku Malawi; ina ikamatuluka, ina imakhala ikulowa, nkhani sizimatha. M’busa wina uku akuyenda chewu chewu kaamba koganizilidwa kuti wakhala akuchita kusaweluzika ndi mkazi wa nkhosa yake yomweso yakhala ikumupatsa chithandizo chochuluka, inde kuluma chala chokudyetsa phalacho.

Nkhaniyi yayambira kutsamba la nchezo la thwita (twitter) komwe tsamba la ‘Accused Number One’ lasindikiza uthenga odandaula omwe mwini nkaziyu analembera m’busa oganizilidwayu.

Malingana ndi zomwe tsamba lino lawona pa masamba a thwita ndi fesibuku (Facebook), m’busa oganizilidwayu ndi a Chancy Mchewere Banda a mpingo wa Seventh Day Adventist (SDA) ku Mtunthama m’bomala la Kasungu.

Muuthenga omwe ukumwazidwawu, mkulu ‘odyeredwayu’ akudandaula kuti wapeza mauthenga a pafoni omwe mbusayo amalumikizana ndi mkazi wakeyo.

Mkuluyu wadandaulaso kuti abusa a Mchewere Banda anapanga chiwembu choti posachedwapa amuthawitsire mkazi wa nkhosa yawoyo mdziko la America.

“Zindikirani kuti mauthenga onse achikondi omwe mwakhala mukulemberana ndi mkazi wanga, ali m’manja mwanga, ndipo zikusonyeza kuti mosakayikira mwasangalala ndi ‘katundu’ wa mkazi wanga mokwanira m’nyumba mwanga.

“Mwamukonda mkazi wanga mpaka kuganiza zomuthawitsira mdziko la America,” wadandaula choncho mkulu ‘odyeledwayo’ muuthenga omwe unalembedwa m’chingerezi.

Akuluakulu a kale sankama akamati gona nkuphe sali patali kaamba koti zadziwikaso kuti mkulu ‘odyeledwa’ mkaziyu anali mmodzi mwa akhilisitu a mpingowo omwe akhala akuthandiza m’busayo ndi zinthu zosiyanasiyana kuphatikizapo zakudya za tswayitswayi.

Iye wati wavomeleza kuti ‘wadyeledwa’ mkazi ndipo wati pano akufuna akamusiye mkazi wakeyo ku nyumba kwa m’busayo koma waopseza kuti abusawo akozekele podziwa kuti mamuna mzako mpachulu.

“Ndinakusamalirani ngati munthu wa Mulungu, ndikukudyetsani zakudya zabwino zomwe simumadya kunyumba kwanu, osadziwa kuti ndikudyetsa njoka, ndipo mutadya chakudya changa mudaganiza zodyaso ‘katundu’ wa mkazi wanga. Uyenera kudziwa kuti ndikulira muntima mwanga, ndikusowa tulo chifukwa ndidadzipereka kuti ndikusamalire mtumiki wonyenga iwe.

“Ndavomereza kugonjetsedwa, mtengeni; Ndikukonzekera kumubweretsa kunyumba kwanu kuti muchepetse zokonzekera zanu zaku America; koma; Konzekerani kukumana nane maso ndi maso,” wadandaula choncho nkuluyo.

Pakadali pano nkhaniyi ili ponseponse mmasamba a nchezo komwe anthu akupeleka maganizo osiyanasiyana.

Follow us on Twitter:

Advertisement