Marinica wati sakutula pansi udindo

Advertisement

Anthu omwe amayembekeza kuti awona m’phunzitsi watimu ya dziko lino Mario Marinica akutula pansi udindo kaamba kakusachita bwino kwa timuyi alemba m’madzi ndipo achule awerenga kaamba koti m’phunzitsiyu wati sangapange chibwana chamchombo lende ngati chimenecho.

Nkhaniyi ikutsatira ntibwi wa zigoli omwe timu yampira wamiyendo ya dziko lino yamwetsetsa pabwalo la masewero la Bingu mumzinda wa Lilongwe pomwe imasewera ndi timu ya dziko la Ijipiti lachiwiri pa 28 Malitchi.

Podziwa kuti mamuna mzako mpachulu, timu ya Ijipiti inabwera chikwanekwane ndipo inaonetsetsa kuti chisoni chomwe chakuta kale dziko lino kaamba ka namondwe wa Freddy chikule zedi pokhaulitsa anyamata a Flames ndizigolo zinayi kwachilowere.

Maseweredwe a timu ya Flames anali osapeleka chikoka kwenikweni ndipo izi zinapangitsa kuti aMalawi ena ayitsike timu yawo yomwe ndikukwera yobwerayo ndipo ena amayimba nyimbo zouza m’phunzitsa watimuyi, Marinica kuti azitaye kaamba koti walephera.

Koma poyankhula ndi atolankhani, Marinica wati sakutula pansi udindo ku timu ya Flames ndipo wati akufuna kuti awonetsetse kuti timuyi ipeze zotsatira zabwino kuchokera mumpikisano wotsatira womwe uyambe mu June mpaka September chaka chino.

Mphunzitsiyu wati sasiya ntchito chifukwa choti anthu mdziko muno akufuna kuti iye atelo ndipo wati adikira kuti kontalakiti yake yomwe ifike kumapeto sabata yoyamba ya mwezi wa April chaka chino, ithe kaye.

“Ine sindine munthu woti nkungosiya ntchito mwachisawawa, apa palibe nkhani. Anthu akungokokomeza. Mu mpira nthawi zina umawina ndipo nthawi zina umaluza ndiye mpira umenewo. Pa nkhani yolephera kukwanilitsa cholinga, zolinga zomwe mukunena inu sizolinga za ine.

“Pali anthu omwe ali ndi zolinga, ine ndilibe cholinga chili chonse mu kontalakiti yanga koma nthawi zina anthu amakhala ndi chiyembekezo chachikulu ndipo zimachitika,” watelo Marinica.

Atafunsidwa ngati nzeru zake za mpira wachangu zikugwira ntchito, mphunzitsiyu wati nzeru zake zikugwira ntchito ndipo anthu awona kusintha ngati apatsidwa mwayi wopitiliza kuphunzitsa Flames kwa nthawi yayitali.

Marinica wadzudzulaso aMalawi chifukwa chosangalalira mphangala ya timu ya Ijipiti yomwe imasewera mu timu ya Liverpool Mohammed Salah zomwe akuti zinawapatsa alendowa mangolomera apaderadera.

“Amalawi ochuluka anatanganidwa kupeleka moto kwa Ijipiti komaso Mohammed Salah zomwe ndi zolakwika ndipo izi ndi khalidwe loipa komaso losakonda dziko lawo,” anaonjezera choncho Marinica.

Pamasewero khumi ndi asanu (15) omwe timu ya Flames yamenya pansi pa ulamuliro wa Marinica, timuyi yangopambana katatu kokha, yalepherana mphavu ndi ma timu ena kasanu (5) ndipo yaluza kasanu ndi kawiri (7).

Tsikuli lidaliso losaiwalika kwa mtsogoleri wa Football Association of Malawi (FAM) a Walter Nyamilandu Manda kaamba koti a Malawi ochuluka ananyamula zikwangwani zomwe zinali ndi mauthenga oti nkuluyu naye atule pansi udindo wake.

Mauthenga mu zikwanganizo amasonyeza kuti aMalawi sakukhutira ndi utsogoleri wa a Nyamilandu Manda ndipo anthuwo ati mkuluyu yemwe walamulira bungwe la FAM kwa zaka zoposela khumi ndi zisanu, apeleke mpata kwa anzake podziwa kuti mlendo amadza ndi kalumo kakuthwa.

Masewerawa atatha, anthu adayamba kuponya mabotolo mkati mwa bwaloli kusonyeza kukwiya ndipo izi zidapangitsa Apolisi aponye utsi wokhetsa misozi kwa ochemelerawa omwe anali kunja kwa zipata za bwaloli.

Follow us on Twitter:

Advertisement