Mtsogoleri aliyese amanunkha fungo loipa losava pelefyumu, watero Nkasa


…wati anthu akudzipha chifukwa alibe chiyembekezo

…wati otsutsa boma anali odzikonda muulamuliro wawo

Atatenga nthawi asanatulutse nyimbo yatsopano, chiyamba kale pamaimbidwe, Joseph ‘Phungu’ Nkasa, wadandaulira munthu amene akuti anatsitsira mpweya dziko lino ponena kuti mtsogoleri aliyese amene dziko lino lakhala naye amanunkha fungo la minyamalo.

Nyimbo yatsopanoyi yomwe mutu wake ndi ‘Tithawire kwa Iye’, yatulutsidwa lachisanu sabata ino ndipo Phungu Nkasa akukamba zinthu zochuluka zomwe zikukhutsa miyoyo ya aMalawi pano.

Poyambilira Nkasa wati ndizokhumudwitsa kuti pano azitumiki a Mulungu akumapezeka akuchita nawo machimo kuphatikiza kumwa mankhwala opeleka nyonga kusubi ndipo wati pena akamaona zomwe zikuchitika ndi azitumikiwa, akumaona ngati akulota.

Iye wadzudzula ma kampani mdziko muno ponena kuti amawatengera a Malawi ku mtoso ngati maliro a njoka pokweza mitengo ya katundu osiyanasiyana yemwe akupangidwa mdziko momwe muno zomwe wati mzosayenera.

Oyimbayu wadzudzulaso akuluakulu otsutsa boma ponena kuti nawo nthawi yaulamuliro wawo anavetsa kunyung’unya anthu mdziko muno ponena kuti anali a kanga ndiwamba komaso odzikonda.

“Nanu otsutsa boma musaombele mmanja, Mukakhala inu ndilibe nanu mnunkhira, pamoyo wanga onse sindinaoneposo anthu odzikonda ngati inu, Mene munali m’boma munalibe chikondi, chuma munasakaza kugawana nokha nokha amzanu ali m’bomamo angofera fungo koma litubvi munabiba ndinu. Chifukwa chakudziva ndikuipa mitima, ma Nyasa ambiri anachoka nanu chidwi, nakuchotsani m’boma kuti mudziwe kuti dziko sila munthu mmodzi ndi la gulu,” yatelo ndime yachitatu ya nyimboyi.

Nkasa yemwe m’mbuyomu wakhala akuyimba nyimbo zochemelera anthu a ndale, wati anthu ochuluka pano anataya chiyembekezo ngati angapeze mayankho pa mavuto omwe akukumana nawo.

Iye wati kukula kwa umphawi, kusowa kwa ntchito, kusowa kwa ndalama, kukwera kwa katundu komaso malonjezo osakwanilitsidwa, ndi zomwe zikupangitsa kuti mchitidwe odzipha ukule kwambiri mdziko.

Pomwe anthu omwe amvera nyimbo ya ‘Tithawire kwa Iye’ akumaona ngati nyimboyi ikupita kumapeto, Nkasa akumabweretsa ndime yomaliza yomwe yautsa mapili pa chigwa potengera zomwe nzira zembe pamaimbidweyu wakambamo.

Nkasa yemwe anamizidwapo kuti apatsidwa galimoto ndi mtsogoleri wa kale wadziko lino a Bakili Maluzi, wati amene anatsitsira mpweya dziko lino analakwitsa kwambiri ponena kuti zimenezo zinapangitsa kuti mtsogoleri aliyese angabwereyo akhale ndi ‘fungo loyipa’

Mozembaitsa, Nkasa munyimboyi watchula mayina a zitsogoleri onse omwe dziko lino lakhala nawo omwe wati onsewa anakhudzidwa ndi mpweya oyipa osava pelefyumu omwe munthu wina anatsitsira dziko lino.

“Yemwe anatsitsira mpweya dziko la Manyasa, ndikuganiza kuti anali wa mkulu matako chifukwa mpaka pano fungo lake la minyamalo, mtsogoleri aliyese amanunkha nalo, Anabwera K anachokapo ndifungo, Anabwera M anachokapo ndifungo, Nabwera B anachokapo ndifungo, Fungo loyipa losava pelefyumu (perfume), Anabwera J anachokapo ndifungo, Anabwera P anachokapo ndifungo, Kunabwera C anthu anazikupizabe, Fungo loyipa losava pelefiyumu,” yatelo ndime yomaliza ya nyimbo ya Nkasa.

L
Kolasi ya nyimboyi, Phungu Nkasa akulangiza anthu mdziko muno kuti athawire kwa Mulungu Yehova yemwe wati ndiye mtsogoleri opanda chinyengo, wachilungamo komaso yemwe amakwanilitsa zomwe walonjeza kusiyana ndi atsogoleri a dziko la pansi.

Pakadali pano anthu omwe amvera nyimboyi akupeleka ndemanga zosiyanasiyana ndipo anthu ena akumuyamikira Nkasa kaamba ka lunso lake makamaka pakapekedwe ka nyimbo.

Follow us on Twitter: