Ayaya amwalira atadwala nsana


Malawi24.com

M’modzi mwa madokotala azitsamba odziwika bwino mdziko muno, mai Bwanali am’boma la Neno omwe amadziwika ndi dzina loti Ayaya amwalira.

Malingana ndi khansala wa dera la Lisungwi m’boma la Neno a Mark Ngwangwa, mai Bwanali amwalira lachiwiri masana pomwe akuti amadwala nthenda ya kupweteka kwa nsana.

Malipoti akusonyeza kuti thupi la malemu Ayaya lilowa m’manda lachinayi mmudzi mwa a Yoyola mdera la mfumu yaikulu Symon m’boma la Neno komwe iwo amachokera.

Mai Bwanali adatchuka kwambiri kaamba kothandiza kwambiri anthu ochuluka mdziko muno komaso mayiko ozungulira ngati Mozambique ndi mankhwala azitsamba kuphatikizapo mankhwala olemeretsa.

Mayiyu anatchukaso kwambiri kaamba ka mphekesera zomwe zinaveka kuti amapeleka chibalo kwa anthu amene asemphanitsa dzizimba pa mankhwala azitsamba omwe iwo ankapeleka.

Mu November chaka cha 2020 dziko lino linatekeseka patabuka mphekesera zoti Ayaya amwali ndipo asiya mawu zoti aliyese amene anakatenga mankhwala azitsamba kwa iwo, apite akagwire bere la mtembo wawo.

Koma patadutsa masiku ochepa, msing’angayu anabwera poyera ndikutsutsa mphekesera za imfa yawo pomwe anayankhula ndi imodzi mwa nyumba zoulutsira mawu mdziko.

Follow us on Twitter: https://twitter.com/Malawi24