“Mukanamva ndamfera mu ring’i!” — walira wankhonya wa ku Malawi atagagadidwa ndi zibakera ku Zambia

Advertisement

Mkwanda (L)

Mawu a malemu pazisudzo John ‘Izeki’ Nyanga oti ‘zina umangowona waziyamba’ akuyankhulidwa mobwelezedwa ndi anyamata atatu osewera nkhonya mdziko muno kwinaku akuziguguda pachifuwa kuti unkalinda izi moyo wanga? Kaamba ka zibakera zomwe agagadidwa ku Zambia zomwe akuti zinawaonetsa dzenje lawo lamanda osati nyenyezi.

Osewera nkhonya atatuwa omwe ndi Mussa ‘Boyker’ Mkwanda, Agness Lewis komanso Yusuf Ali, anatenga nawo gawo pa mpikisano wankhonya omwe unakozedwa ndi Team Sting Boxing Promotions ndipo unachitikira mdziko la Zambia kumathelo asabata yatha.

Koma huu! Mphuno salota, atatuwa omwe si anthu wamba kumbali ya nkhonya mdziko muno, awona mbonawona pomwe athibulidwa mosaveledwa chisoni ngati galu wa misala ndi mizwanya imzawo pa nkhonya.

Lamulungu lapitali, Mussa Mkwanda wagagadidwa ndi Mbachi Kaonga ndipo iye sanadikile kuti nkhonyayi ifikeso mpaka gawo lomaliza la chisanu ndi chitatu (8 round) koma anaimika manja nkhonyayi ili gawo lachiwiri ponena kuti anakati akakamile kupitiliza ndewu yandalamayo, anakatha kubzala chinangwa.

Iye anauza nyuzipepala ya The Nation kuti anaona kuti ndi kwabwino kupulumutsa moyo kaamba koti chibakera chilichose cha Mbachi akuti chimamveka ngati muja amachitira mabvu nkhomola ndipo wamutaila kamtengo mzakeyo kuti ndi chitsa chotsala mu lupsa.

“Ndikuyenera kuvomereza kuti amene ndimamenyana naye sanali munthu wamba. Anakandipha kaamba koti pafupifupi chibakera chake chili chonse chomwe amaponya, chimandionetsa zakuda. Unali usiku oyenera kusakumbukilidwaso.

“Mpakana zinafika pena poti ndinaona kuti kupulumutsa moyo wanga chinali chinthu chokhacho chofunika kwambiri paine. Ichi nchifukwa chake ndinangoimika manja kuti ndalephera,” anatelo Mkwanda pouza nyuzipepala ya The Nation.

Mbali inayi Agness Lewis wapandwa ndi mtsikana mzake waku Zambia yemwe dzina lake ndi Violet Phiri ndipo katswiri wa nkhonya waku Malawi yu sanadikileso gawo lachiwiri ngati Mkwanda kaamba koti iyeyu anaona ziphaliwali za zibakera mu gawo loyamba ndipo anapukusa mutu opanda nyanga kuti sakwanitsa patangotha masekazi 23 (23 seconds) masewerowo chiyambileni.

Mwa akatswiri ankhonya atatu aku Malawi wa, amene anaonetsako chamuna ndi Yusuf Ali yekha kaamba koti ngakhale wagonja nkhonya yake kudzera mu mapointi, ma lipoti akusonyeza kuti anaswana koopsa ndu Gracious Simwalizi ndipo anali ndimwayi waukulu oti anakapambana.

Ndipo poyankhula ndinyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno, mphunzitsi yemwe ali ndi osewera atatuwa mdziko la Zambia, Ronald Metazama, wati ngakhale sizinayende osewerawa anayesetsa ku chilimika kumbali yawo.

Follow us on Twitter:

Advertisement