Oyimba Tuno wati abambo akumaveka mphete mah*le

Advertisement

M’modzi mwaoyimba achizimayi odziwika bwino mdziko muno Tunosiwe Mwakalinga, yemweso anakhalapo chiphadzuwa cha mzinda wa Blantyre, wakwiyitsa azibambo pomwe wawanena kuti ambiri mphete zawo anaveka azimayi ogulitsa matupi.

Mwakalinga yemwe amadziwika bwino kwambiri kuti Tuno lomwe ndi chidule cha dzina lake, anashosha kudambwe pomwe musabatayi analemba patsamba lake lamchezo la thwita kuti “Koma ma ring (mphete) mukuveka mahule guys.”

Izi zinakwiyitsa azibambo ochuluka omwe anaona zolembedwazo omwe kenaka anakhamukila patsambali ndipo anayamba kubweza moto, kumulavulira oyimbayu mawu achipani.

Munthu wina yemwe dzina lake ndi Young MDonald sanapsatile mawu koma kumuuza oyimbayu kuti naye alimugulu la azimayi ogulitsa matupi omwe akunenedwawo, ndipo analemba kuti “Ngati akuveka mahule iwe sakuveke bwa?”

Koma poti nthawi zambiri nkhonya yobwezera imanyung’unya zedi, zomwe anayankhula MDonald zinamudinya Mwakalinga yemwe analephera kuwugwira mtima ndipo anayankha kuti; “Ndekuti sindili mugulu la mayako. Si nawonso anavekedwa.”

Kwa anthu omwe anakhamukira ku tsambali, zinali ngati akuonera filimu ya nkhondo yomwe omenyanawo amasinthana zipolopolo mopanda chisoni, ndipo bomba limaponyedwa koma poti akita samafa, umamuona wadzukaso ngati momwe anapangira Tuno.

Oyimbayu anapitilirabe kuchita makani ngati ofula agalu ndipo anapitilira kubweza moto kwa anthu omwe anakhamukira ku tsambali, komabe podziwa kuti muumodzi muli mphamvu, oyimbayu anagonjetsedwa ndipo kenaka umunthu wake utabwelera, anafufuta zomwe analembazi.

Pakadali pano anthu adzudzula oyimbayu yemwe chaka chatha wapambana mphoto ngati oyimba wachizimayi yemwe waposa onse mumpikisano wa Maso, kuti akuyenera akhale ndikhalidwe la bwino komaso apewe kuyankhula zinthu zomwe zingakwiyitse anthu omutsatira.

Follow us on Twitter:

Advertisement