Yambani kulongedza ife tidzakonze zinthu, Kabambe wauza a Chakwera

Advertisement

M’modzi wa anthu omwe akufuna utsogoleri ku chipani cha DPP a Dalitso Kabambe awuza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti ayambe kulongedza popeza kuthekera kokonza zinthu alibe.

Malingana ndi a Kabambe omwe anakhalapo mkulu wa bank yaikilu ya Reserve, iwo ali okonzeka kuzakonza zinthu m’dziko muno.

Mukulemba kwawo pa tsamba la mchezo m’mawa uno, a Kabambe ati mavuto omwe alipo m’dziko akupangitsa kuti kusabwele anthu ndi makampani odzayambitsa ma bizinesi akuluakulu.

Iwo anapereka chitsanzo cha kuvuta kwa magetsi kuti kukupangitsa kuti anthu asabwere ndi ndalama zawo ku Malawi kuno poti akumaona kuti boma la Malawi silikulabadira za magetsi.

A Kabambe anaonjezera kunena kuti akuba tsopano angochita m’mene akufunira ku Malawi kuno zomwe zikufooketsa ngakhale anthu ochita bizinesi a komwekuno.

Vuto lina lomwe anatchula a Kabambe ndi tsankho komanso katangale. Iwo anati anthu a bizinesi ngakhale a komwekuno sakupatsidwa bizinesi ndi boma ndipo m’malo mwake adindo akumachita kukasaka anzawo a mayiko ena kuti agawane chuma cha boma la Malawi.

“Zinthu zonsezi izi ma investor amene mumawayitanirawo amazidziwa. Pamaso amatipatsa chiyembekezo koma tikatembenuka basi file yathu amayitaya.

“Mmalo mwa ma investors a phindu kumabwera ma kampani opanda ofesi, ma dobadoba ndi atambwali basi. Akatero koma atsogoleriwo ndiye mpaka misonkhano ya atolankhani kusangalalira bodza limeneli.

“Konzani kaye business environment kenako muzipita kukayitana ma investor. Koma poti kuthekera kokonza zinthu mulibe, ndiye yambani kulongeza kuti a mzanu tizakonze zimenezo,” anatero a Kabambe.

A Kabambe akufuna utsogoleri wa chipani cha DPP kuti azayimile chipanichi pa zisankho za pulezidenti za mu 2025. A Chakwera akuyembekezereka kuzapikisana nawonso pa zisankhozi.

Follow us on Twitter:

Advertisement