Chakwera asiya Malawi pamoto wa ku Iguputo

Advertisement

Ulendo wa ku Kanani walephereka. Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wasiya Malawi akulira ndikuphula njerwa za moto. Chakwera  yemwe anayenda mwakachetechete kuopa kuwowozedwanso ku Lilongwe akuti wafika bwino ku Iguputo.

Lachisanu, a Chakwera anawowozedwa pamene amadutsa pa malo othilira mafuta pomwe gulu la a anthu linaunjikana kudikira kugula mafuta.

Dzulo popita ku Iguputo a Chakwera anayenda mwakachetechete, osaliza sayilini ndipo aMalawi akuona kuti mtsogoleriyu amaopa kuwowozedwanso.

Kupatula vuto la mafuta, aMalawi aphinjikanso ndi vuto la kuthimathima kwa magetsi, kukwera kwa mitengo ya zinthu ndi kusowa kwa ndalama za kunja.

Izi zikuchitika pomwe boma likukanika kuyendetsa bwino zinthu ndipo ndalama zikungobedwa. Posachedwapa, zinaululika kuti boma linabetsa ndalama zokwana K750 million zomwe zinapekekedwa mwachinyengo ku kampani ina yaku UK.

Pamasamba a mchezo aMalawi akudandaula kuti a Chakwera akuwaphulitsa anthu njerwa za moto m’malo mopita nawo ku Kanani.

Padakali pano, a Chakwera ali ku Iguputo komwe akuyembekezera kukhala nawo pa msonkhano wa chilengedwe.

 

Follow us on Twitter:

Advertisement