Siyani kudya gondolosi musanakule – APM

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika wauza achinyamata kuti asamadye nawo gondolosi pofuna kuonjezera mphamvu. Iye wanena izi pa mwambo wa Mulhakho wa Alhomwe kwa Chonde mu boma la Mulanje.

Polangiza achinyamata kuti akhale ndi moyo wautali monga iye, Mutharika anati achinyamata asiye kugwiragwira.

“Ine ndinafika pano chifukwa cha zinthu zingapo. Ndimapewa kugwiragwira, mowa komanso chamba,” anatero Mutharika. Ndipo anaonjezelapo pokamba nkhani ya gondolosi.

“Ndamva kuti achinyamata a zaka 15 ndi 16 akumagula gondolosi. Iyayi musiye zimenezo. Mudikire kaye mukakula kuti mugule gondolosi,” anatelo Mutharika.

Mitengo ya gondolosi imakhulupiliridwa kuti ili ndi kuthekera koonjezera mphamvu mwa abambo. Mwambo wa Mulhakho wa Alhomwe umatengedwa ngati ndi kumene anthu ochuluka amakapezako gondolosi.

Pa mwambo omwewu, Mutharika anayankhulapo pa ndale za mu chipani cha DPP chimene iye akutsogolera.

Ndemanga zake pa ndale zapangitsa ena kudzudzula Mutharika

Advertisement