Alibe moto Chakwera, anthu atopa naye – atelo a Katswiri a kafukufuku


Chikomekome chamkuyu…

Ngati alipo anthu akugomelabe utsogoleri wa Chakwera ndiye ndi kutheka ndi a pa banja pawo ndi nduna zawe zokha basi. Mwina ndi a Yufi owelegeka. Chifukwa kafukufuku waonetsa kuti pa a Malawi handede alionse, khumi okha ndiwo akupatsidwa chilimbikitso cha mphamvu ndi utsogoleri wa abusa a Chakwera.

Malinga ndi zotsatila za kafukufuku amene bungwe la za kafukufuku la Afrobarometer lidachita mu dziko muno kumayambililo kwa chaka, a Malawi ochuluka ataya chikhulupililo mwa mtsogoleri wa dziko linoyu.

Lipoti limene a bungweli atulutsa, ati a Malawi osapyola khumi pa handede alionse ndiwo ali ndi chikhulupililo chothelatu mwa utsogoleri wa a Chakwera. Pamwamba pa amenewa, aliponso a Malawi osakwana makumi awili (20) pa handede alionse amene akukhulupilila a Chakwera.

Pamene anthu ochepa chonchi ali ndi chikhulupililo pa a Chakwera, kafukufuku’yu anapeza kuti a Malawi ochuluka alibiletu chikhulupililo mwa kuthekela kwa a Chakwera. Anthu oposa 51 pa handede ati iwo sakuonapo kanthu ka utsogoleri mwa a Chakwera. Anthuwa akutsagana ndi ena ongochepela pang’ono pa 15 pa handede alionse amene nawo alibe chikhulupililo mwa a Chakwera.

Anthu ochuluka nawo akuona kuti dziko la Malawi pansi pa a Chakwera likungoyenda ngati nkhuku yodulidwa mutu. Lilibe komwe likulowela. Malinga ndi kafukufuku uyu, a Malawi ambili akuona kuti a Chakwera akanika kulondoloza chuma cha dziko lino.

Anthu amene anafunsidwa maganizo, anavomelanso kuti ochuluka mwa iwo alibe chikhulupililo mu chipani cha Kongeresi ngakhale cha UTM. Iwonso koma ananenapo kuti sakudalila kwenikweni zipani zotsutsa.

Kukanidwa kwa a Chakwera kunadza pamene nkhondo yolimbana ndi katangale imaoneka kuti ilibe tsogolo. A Chakwera akhala akudzudzulidwa pakukanika kwawo kuthana ndi katangale.

A katswiri ena otsata za kafukufuku ati atachitika tsopano kafukufuku otele, anthu ochuluka kwambili atha kukana a Chakwera. Iwo ati kugwetsa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha kumene lidachita boma la a Chakwera komanso kuthimathima kwa magetsi kutha kukhala zina mwa zifukwa zimene a Malawi angakanile kwa m’tu wagalu a Chakwera.

One comment on “Alibe moto Chakwera, anthu atopa naye – atelo a Katswiri a kafukufuku

  1. Kafukufuku wanu ngwaboza akuyimira a Malawi aulesi, ife ngati alimi zathu zili bwino kumbewu ku zoweta, amene mukuwafunawo amapondereza ife alimi

Comments are closed.