Zilikoliko 2025: Mutharika, Chikomeni awonetsa chidwi chodzaimanso

Advertisement

Pamene masiku akuthera kuchitseko kuti dziko lino lizachititse chisankho china mu 2025, Ras David Chikomeni Chirwa walengeza kuti adzapikisana nawo pomwe mtsogoleri wakale a Peter Mutharika ati anthu ambiri akuwapempha kuti adzaimeso.

Nkhaniyi yayamba ndi a Mutharika omwe la mulungu pa 10 July anauza wailesi ya Voice of America kuti a Malawi ambiri kuphatikizapo atsogoleri amipingo komanso mafumu akuwapempha kuti adzapikisane nawoso pampando wa mtsogoleri wadziko pa chisankho chamu 2025.

Mtsogoleri wakale wa dziko linoyu wati magulu a anthu omwe anakumana nawo posachedwa pankhaniyo, awauza kuti iwo ndi omwe angazakwanitse kumalizitsa zitukuko zomwe akuti boma lapano likulephera kutsilizitsa.

“Ndinatulutsidwa m’boma patangotha chaka chimodzi, ndinali ndizaka zinayi zoti ndilamulire koma ndinatulutsidwa, choncho anthu ena akuganiza kuti ndikuyenera ndimalizitse nthawi yanga kutiso zitukuko zomwe ndinaziyamba zomwe boma lapanoli likukanika, zithe.

“Anthu ena akufuna ndibwelere ndipo ndakhala ndikupemphedwa zimenezo. Masanawa ndimakumana ndi atsogoleri azipembedzo komaso mafumu omwe amandipempha kuti ndizaimeso mu 2025 ndipo ndi chifukwa chake ndinalephera kuyankha foni yanu,” anatelo a Mutharika poyankhula ndi wailesi ya Voice of America.

A Mutharika omwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP, ati pakadali pano sanayankhe pazomwe anthu akuwapemphazi ponena kuti akufuna adye kaye mutu ndipo ati mtsogolo muno ndi pamene alidziwitse dziko chiganizo chawo pamapemphowa.

Patangodutsa maola ochepa chabe a Mutharika atayankhula izi, Ras
Chikomeni Chirwa yemwe analephera kuimira pa zisankho za 2019 kaamba kolephera kupereka K2 million ku bungwe loyendetsa zisankho la MEC, wati wapanga chiganizo choti adzaimeso mu 2025.

Chirwa

Iwo anauza imodzi mwa nyumba zofalitsa nkhani mdziko muno kuti akukhulupilira kuti chisankho cha mu 2025 chitha kudzawakomera iwowo ndipo ati panthawiyi, iwo adzasankhaso mayi awo a Catherine Nyness Kayange ngati wachiwiri wawo.

Follow us on Twitter:

Advertisement