Ndakufikitsani ku Canaan — Chakwera

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anena kuti akwanitsa kale kuchita zambiri zomwe iwo anawalonjeza a Malawi mu nthawi ya kampeni.

A Chakwera anena izi lero ku nyumba ya chifumu ya Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo omwe amalandila ndalama kuchokela ku African Development Bank.

Malingana ndi a Chakwera, iwo analonjeza za ulamuliro wabwino komanso kuwalola mabungwe a boma kugwira ntchito zawo mosafinyika malingana ndi malamulo zomwe anati zikuchitika.

Iwo anatinso boma lawo ladzala zitukuko zosiyanasiyana mu madera m’dziko muno ndipo izi zayanjanitsa a Malawi.

A Chakwera ananena izi ngakhale pali zambiri zomwe iwo analonjeza koma sanakwanilitse.

Zina mwa zomwe a Chakwera analonjeza koma sizinachitike ndi monga kumanga sukulu za sekondale zapamwamba, kutsekula minda ikuluikulu, kumanga mizinda yasekondale, kutsitsa mitengo ya ma pasipoti komanso kuchotsa mtengo wolumikizitsa magetsi.

Follow us on Twitter:

Advertisement

2 Comments

  1. I think Mr President akulota atakwanitsa poti kulota saletsana akungoyenera kutero

Comments are closed.