A Chakwera sanauze Ukraine ndi Russia kuti azimenyana, atero a Mkaka


Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Eisenhower Mkaka ati mavuto ena omwe anthu m’dziko muno akukumana nawo anayamba chifukwa cha nkhondo ya pakati pa Ukraine ndi Russia ndipo ndikulakwa kumanena kuti mavutowa abwera ndi Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera poti a Chakwera sanauze Ukraine ndi Russia kuti azimenyana.

A Mkaka omwenso ndi nduna yoona za kusintha kwa nyengo ananena izi ku Mitundu ku Lilongwe lachisanu pomwe a Chakwera anapangitsa msonkhano wa ndale.

A Mkaka anati ku Malawi mavuto alipodi koma pali ena akufuna kumanamiza mtundu wa a Malawi kuti mavutowo anabwera ndi a Chakwera.

A Mkaka anati mavuto a kukwera kwa mitengo ya zinthu ali pa dziko lonse ngakhale ku Amerika ndi ku Mangalande.

Iwo anaonjezera kuti pa dziko lonse la pansi pali mavuto a Covid ndipo ku Malawi kuno kunalinso vuto la kusefukira kwa madzi.

“Zinthu zija zaononga kwambiri, milatho, misewu zonse kupita ndiye kuti inuyo bwana mukuyenera kuyambiranso [kumanga],” anatero a Mkaka.

Kenako ananena za nkhondo ya pakati pa Russia ndi Ukraine kuti yabweretsa mavuto a kukwera kwa mitengo ya zinthu monga fetereza, tirigu ndi mafuta.

“Bwana, nkhondo ya Russia ndi Ukraine inu sikukukhudzani ayi. Palibe tsiku limodzi lomwe inu mudalankhula kuti kamenyanani ku Ukraine,” adatero a Mkaka.

A Mkaka anati chinthu chabwino ndi chakuti a Chakwera akuvomereza za mavutowa ndipo chipani cha MCP chili pa mbuyo pa a Chakwera kuwathandiza kuthana ndi mavutowa.

Iwo anayamikiranso a Chakwera popitiriza kupanga zitukuko ngakhale pali mavuto.

2 thoughts on “A Chakwera sanauze Ukraine ndi Russia kuti azimenyana, atero a Mkaka

Comments are closed.