A Malawi akaona wapolisi amaona katangale – waulula kafukufuku

Advertisement

Zoti mayiko ena akaona wapolisi amaona mfuti, kapena anthu okhazikitsa chitetezo ndi zakomweko. Kuno akuti timakhala taona ngwazi za katangale.

Kafukufuku amene bungwe la Afrobarometer wachita, watsimikiza kuti unyinji wa a Malawi ulibe chikhulupililo mu polisi yathu. Malinga ndi kafukufuku uyu, a Malawi ochuluka kwambili akuona ngati a polisi ochuluka ngakhale onse amene ali ndi mzimu wa katangale.

A Afrobarometer mu kafukufuku wawo anapenzanso kuti a Malawi 83 pa 100 alionse amaopa kuti akaulula za chinyengo zomwe zikuchitika, ochita zachinyengowo angathe kufuna kuthana nawo.

Koma poyankhulapo dzulo pa mwambo wokhudzana ndi zakatangale ku Mzuzu, mkulu wa bungwe lothana nid katangale la ACB, a Martha Chizuma, anati ndikofunika kuti anthu adzinena chilungamo pa nkhani zakatangale.

Wachiwiri wa mtsogoleri  wa dziko lino a Saulos Chilima analimbikitsanso a Malawi kuti azikanena ku ACB akaona za katangale zikuchitika.

Advertisement