Konzekani, kukubwela mvula ndi mphepo zoononga – a za nyengo


Akatswili a zanyengo ati kuyambila lachitatu sabata lino, kubwela mvula ya mkuntho yoononga katundu.

Malinga ndi chikalata chimene atulutsa ndipo chasainilidwa ndi mkulu wa nthambi yoona za nyengo mu dziko muno, a Jolam Nkhokwe, mvula ya mkunthoyi iyambila chigawo cha kummwela.

Uthenga mu chikalatachi wati mvula imeneyi ikhala ikupambadza mpaka kufikila lamulungu, pa 28 November.

“Izayambila chigawo cha kummwela, ndi kumapita mpaka kufika pakati,” atelo Akatswili odziwa za nyengo.

Iwo anena kuti ukali wa mvula iyi uli ndi kuthekela koononga nyumba ndi kusasula ma ofesi amene. Ndipo apa achenjeza anthu kuti aonetsetse kuti tsindwi zawo ndi zolimba.

Kupatula mvula ya mphamvu ndi mphepo ya mkuntho, ati kuchitika ziphaliwali ndipo anthu akumemedwa kuziteteza.