Anthu akugonera mango kuno, Phungu wa ku Balaka wauza a Chakwera

Advertisement

Phungu wa ku Balaka West, Bertha Ndebele, wauza Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti anthu ku dera lake akugonera mango chifukwa chakusowa chakudya.

A Ndebele, omwe ndi a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) amayankhula izi kwa Phombeya ku Balaka pomwe a Chakwera pamodzi ndi mtsogoleri wa dziko la Mozambique a Filipe Nyusi amatsekulira pulojekiti ya ntchito za mphamvu za magetsi yomwe ikuthandizira kuti Malawi izitapa magetsi ku Mozambique.

Malingana ndi a Ndebele, ku dera lawo kumavuta njala ngakhale mvula ibwere, anthu sakolola zakudya zokwana.

“Moti anthu ali ukowo ambiri mwa iwo sanakolole olo thumba limodzi la chimanga. Ngati akudya kuti akugona adya, ndi mango. Nkhawa ndi yakuti mango akutha ndiye sakudziwa kuti adya chani,” anatero a Ndebele.

A Ndebele anapempha Chakwera kuti iwo ngati Mtsogoleri wa dziko athandize anthuwa kuti apeze chakudya kuti akwanise kulima ndipo azakolole chaka cha mawa.

Iwo anadandaulanso kuti ku dera lawo kulibe chipatala cha boma ndipo anthu amachoka kumeneko kupita ku Balaka District Hospital komwe kuli chipatala cha boma poti zipatala zomwe zili pafupi ndi zolipira.

Apa iwo anapempha boma kuti limange zipatala zing’onozing’ono ziwiri mu derali.

Poyankhapo, a Chakwera anati boma lizipereka chithandizo cha chakudya mwansanga.

“M’malo momadikilira kuti tikafike pa January, madera ena ngofunika mathandizo aziyamba mwansanga chifukwa pamakhala kusiyanasiyana mu zosoweka pakati pa anthu,” anatero a Chakwera.

Pa dandaulo la zipatala, a Chakwera anati  ndi cholinga cha boma lawo kuti lipititse zipatala komwe kuli anthu.

 

 

 

Advertisement