Zitsulo kunolana: A Muluzi awuza a Mutharika kuti athetse mpungwepungwe mu DPP

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi alangiza mtsogoleri wakale a Peter Mutharika omweso ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP kuti ayese kuthetsa kusagwirizana komwe kulipo mchipanichi.

A Muluzi ayankhula izi Lamulungu pa 10 October kwa Chonde m’boma la Mulanje pomwe amamalizitsa nawo mwambo wa Mulhakho wa Alhomwe omwe unayamba Lachisanu pa 8 October.

Iwo anati ndizokhumudwitsa kuti mumchipanichi muli kusagwirizana makamaka pankhani ya utsogoleri zomwe anati zitha kupangitsa chipanichi kusapambana pachisankho chomwe chidzachitike mchaka cha 2025.

Mtsogoleri opumayu yemwe amadziwika ndi dzina loti ‘a Chair’ anati a Mutharika pokhala yemwe akutsogolera chipanichi pano, sakuyenera kungokhala chete pemene zinthu sizili bwino mu chipani chawo.

Apa a Muluzi anauza a Mutharika kuti apeze njira zothetsera kusagwirizana komwe kulipo mchipanichi ndipo atinso amene sakufuna chipanichi akuyenera kutuluka mwaulemo osati kubweretsa chipwilikiti.

“Olemekezeka, inu ngati mtsogoleri wa chipanichi, munthu amene mumakhulupilira kuti mumasunga mwana wina aliyese m’Malawi muno, muonetsetse kuti muli mgwirizano mu DPP.

“Nyumba imene imakhala yogawikana ingawine chisankho? Olemekezeka inuyo mutenge ulamuliro onse ndi cholinga choti musakhale kugawikana muchipani chanu,” atelo a Muluzi.

A Muluzi omwe anati samafuna kumayankhula mopsatira anati ubwino wake ndioti kunthambi, kumadera a phungu komaso kumaboma konse kuli bwino kwangovuta ndikumtunda kokha zomwe anati sizovuta kukonza.

Ndipo m’mawu awo, a Mutharika omwe anali mlendo olemekezeka pa mwambowu anati awonetsetsa kuti mgwirizano ulipo mchipanichi ndipo anatiso chipanichi sichingakhale ndi atsogoleri awiri.

Iwo auza onse omwe akukhudzidwa pankhani yakusagwirizana pankhani ya ulamuliro mchipanichi kuti ngati akufuna kukhala mtsogoleri achipanichi adikile msonkhano waukulu omwe akuti udzachitika mchaka cha 2023.

“Pakufunika mgwirizano wabwino, chipani chimodzi komaso mtsogoleri mmodzi. Nonse amene mukufuna utsogoleri wa chipanichi dikirani nthawi idzafika koma pakadali pano vomerezani kuti ndine mtsogoleri wa chipanichi, anatero a Mutharika.

Pakadali pano, a Mutharika anenaso kuti iwo adzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa chipanichi nthawi yomwe msonkhano wankulu udzachitike.

 

Advertisement