‘Kulibe mpungwepungwe mu mgwirizano wa Tonse’

Advertisement

A kunyumba ya boma atsutsa mphekesera zoti mu mgwirizano wa Tonse muli mpungwepungwe.

Nkhaniyi ikutsatira manong’onong’o omwe akhala akumveka makamaka pamasamba amchezo oti akuluakulu azipani zomwe zili mugwirizanowu sakumwerana madzi kaamba kosepmhana chichewa pazinthu zina.

Manong’onong’owa anaphelezera sabata yatha pomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima anapempha anthu otsatira zipani zomwe zili mu mgwirizano mchigawo chakumpoto kuti apitilize kukhala anthu ogwirizana.

Kanema yemwe wafala pamasamba amchezo, akuonetsa a Chilima ndi akuluakulu ena amgwirizanowu atagwada pansi kupempha kuti mumgwirizanowu mukhale kukondana ndipo anauzaso anthu kuti: “tsiku loponya voti pa 23 June chaka chatha tinali limodzi ndiye wina asayambe kutumbwa lero.”

Koma malingana ndi Brian Banda yemwe ndi oyankhulira a Chakwera, mphekesera yoti mu Tonse muli ming’alu ndiyabodza ndipo watsutsa mwa ntu wagalu kuti mumgwirizanomu muli kukokana mataye.

Banda yemwe Lolemba amayankha mafuso kuchokera kwa atolonkhani ku nyumba yachifumu ya Sanjika mumzinda wa Blantyre wati omwe akufalitsa nkhaniyi akungofuna kuwononga ubale wabwino omwe ulipo pakati pa akuluakulu a mgwirizano wa Tonse.

Iwo ati akuluakulu onse a mgwirizanowu omwe ndikuphatikizapo mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera komaso wachiwiri wawo a Chilima, amakumana pafupi pafupi zomwe ati ndichisonyezo kuti ubale wawo onsewa ulibwino.

Poyankhapo pa zomwe anayankhula a Chilima pomwe anali ku mpoto sabata yatha, Banda wati zomwe anayankhula wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko linoyu sizikutanthauza kuti mu mgwirizano wa Tonse kuli nkhondo koma wati a Chilima amangofuna kulimbikitsa umodzi pakati anthu otsatira zipani zomwe zili mumgwirizanowu.

“Chilichonse chili bwino mum’boma la Tonse, mulibe kugawanika. Zomwe amanena a Chilima pomwe anali mchigawo cha kumpoto, linali pempho chabe kwa otsatira mgwirizanowu kuti akuyenera onse kugwilira ntchito limodzi, osati zomwe anthu akufalitsazi.

“Mutha kuona kuti palibe vuto lili lonse pankhani ya atsogoleri adziko lino. A Chakwera, a Chilima komaso atsogoleri onse amumgwirizano wa Tonse amakumana pafupi pafupi ndikumakambirana zinthu zosiyanasiyana zomwe zikusonyeza kuti kulibe zokokanakokana zomwe anthu akufalitsazo,” watero Banda.

Iye anabwereza mawu omwe anayankhula a Chakwera posachedwapa kunyumba ya malamulo kuti ngati pali anthu ena omwe akudikilira kuti mgwirizano wa Tonse ugawanike, ayiwale zimenezo ponena kuti mgwirizanowu siungagawanike.

Posachedwapa panatuluka nkhani yoti nduna ya zachitetezo cha mdziko a Richard Chimwendo Banda pamodzi ndi akuluakulu ena achipani cha MCP anamenyedwa ku mpoto ndi anthu omwe amaganizilidwa kuti ndi otsatira chipani cha UTM ndipo izi zinabweretsa mafuso ochuluka paubale wa zipani zomwe zili mgwirizanowu.

Advertisement