CAMA yaikira kumbuyo boma pankhani ya mitengo ya yamafuta


Bungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula mdziko muno la Consumers Association of Malawi (CAMA) layikira kumbuyo boma pankhani ya mitengo ya mafuta a galimoto.

Nkhaniyi ikutsatira zionetsero zomwe zinachitika mkati mwa sabata ino pomwe madalaivala a maminibasi, makondakitala komaso anthu ochita kabanza wanjinga zamoto amanyanyala ati pofuna kukakamiza boma kuti litsitse mtengo wa mafuta agalimoto.

Anthu wa auzaso boma kuti ngati likane kutsitsa mtengo wa mafutawu, liwaloreze kuti azinyamula anthu atatu pa mpando waminibus zomwe boma latemetsa nkhwangwa pamwala kuti silingachite.

Koma poyankhulapo pankhaniyi, wapampando wa bungwe la CAMA a John Kapito ati ndizokhumudwitsa kuti chipani chotsutsa boma cha DPP chikufuna kulowetsa ndale pankhani ya mafuta agalimotowa.

A Kapito ati boma kuti litsitse mafuta silimangodzuka koma limayamba laona kaye mmene mitengo yazinthu ikuyendera pansika choncho ati sakuona vuto kwenikweni pamitengo ya mafuta yomwe ikugwiritsidwa pano.

Iwo anaonjezera kuti anthu andale makamaka achipani chotsutsa amakomedwa kuuza anzawo olamura zoyenera kuchita chonsecho iwowo ali m’boma momwemo analephera kuchita zomwe akuwuza anzawozo.

“Zimati zikachitika za mitengo ya mafuta, amakhala patsogolo kunena kuti iwowo atakhala kuti ali m’boma anakatsitsa mitengoyo koma chimene chimadabwitsa mchoti amati akakhala kuti tsopano ali mb’omamo palibe chomwe amachita. Izizi zimachitika pokhapokha akakhala kuti achoka m’boma.

“Nkhani ya mitengo ya mafuta choti a Malawi adziwe anthu amenewa asanatisokoneze mitu yathu nchakuti, amagula mafutawa ndi makampani omwe amagulitsa mafutawa ndipo ndalama yapamwamba amaonjezera ndi aphungu imene ili misonkho. Ndi a phungu omwewo amene anakhazikitsa malamulo ndi misonkho kuonjezera pa ndalama ija ndipo pamtengo wa mafuta omwe timalipira panopa, theka yamtengowo ndimisonkho yomwe zinakhazikitsa nduna ndi aphungu,” watelo Kapito.

A Kapito apempha aphungu anyumba ya malamulo kuti akakumana posachedwapa apange zoti achotse misonkho pamitengo yakatundu wina yemwe anati amapangitsa kuti mitengo ya mafuta agalimoto ikwere.