Chonde, musamwe zitsamba pothana ndi covid – a Dokotala akutelo

Advertisement
Covid-19 blue gum steam
Bulugama, kaya mandimu oonjeza, mwinanso soda osakaniza ndi khungwa la mtengo wa muwawani ndinso aloe vera ndi zina ndi zina ati muzisiye kaye. Zikukupwetekani izo zija osati kukuthandizani ku nkhondo yolimbana ndi corona.
Mkulu amene akutsogolera nkhondo yolimbana ndi kuthana ndi kachilombo ka corona kuno ku Malawi, Dr. Phuka achenjeza a Malawi kuti mchitidwe omwa zitsamba pomati ndi njila yoonjezela chitetezo m’thupi maka akapezeka ndi corona ndi oipa ndipo anthu asiye.
Malinga ndi a Phuka, anthu ambili akumapita ku chipatala atavulala kamba ka zitsamba zomwe akumwa akapezeka ndi matenda a Covid-19.
Mu chikalata chimene analemba a Phuka polengeza za momwe zilili ndi corona mu dziko muno anadandaulila mtundu wa a Malawi kuti mcitidwe okumwa zitsamba ukuika miyoyo ya anthu ochuluka pa chiopsezo.
“Ambili sitikudziwa kuti muli chani mu zitsamba izi, zina mwa zitsamba zimenezi zimaononga chiwindi, zina si zabwino kwa impso zathu. Anthu akadwala akumathamangila zimenezi koma sikuti ndi zothandiza, zikupweteka anthu mmalo mwake,” analemba modandaula a Phuka.
Ndipo dotolo wina a Titus Divala ati anthu akapezeka ndi Covid sakuyenela kudalila mu zitsamba.
“Pitilizani kukhala umo mukhalila, koma onetsetsani mukuteteza ena. Imwani madzi ochuluka, chitani masewelo olimbitsa thupi (tionjezelepo tokha: osati kulemetsa thupi), ndipo uzani onse munakumana nawo kuti nawo akhale moziteteza,” analemba pa makina a Intaneti a Divala.

“Ngati mungayambe kutsokomola kamba a Covid, imwani mankhwala a chifuwa amene mumamwa nthawi zonse. Koma mukayamba kumva kubanika komanso ululu mu chifuwa ndiye thamangilani ku chipatala,” anatsindika motelo.

a Malawi ambili ayamba kumwa zitsamba pofuna kuziteteza ndi kuchila kumene kumatenda a Covid amene apha anthu ochuluka pa dziko lapansi.

Advertisement