Danzi lilibe mankhwala? Bodza. Anduna apita ku India kukachila ku Danzi


A boma akuti anachoka mu dziko muno kuti akapeze chithandizo pa vuto la mwendo lomwe anali nalo. Eni ake akuti anakasaka chithandizo pa Danzi lomwe likuwavuta koma ndalama zake lalipila si boma. Mu zithunzi, ukuoneka ndi mutu omangidwa ma bandechi osati mwendo ayi.

Nduna ya zamasewero a Ulemu Msungama yadabwitsa a Malawi kutamveka ma lipoti oti ili mu dziko la India kusakasaka chithandizo choti ichile ku ‘matenda a danzi’.

Malinga ndi malipoti, a Msungama anachoka mu dziko muno ma sabata awiri apitawo kupita ku chipatala mu dziko la India. Nduna za boma zinauza atolankhani kuti a Msungama anatumizidwa ku chipatala ku India kuti akapezeko chithandizo pa vuto la mwendo. Zinatsimikiza kuti ulendo wawo unalipilidwa ndi boma.

Koma chadabwitsa anthu ndi zithunzi zimene zatuluka kuonetsa a Msungama ali ndi mutu wa mu ma bandechi kusonyeza kuti chithandizo chimene alandila ndi cha m’mutu.

Zithunzizi zapangitsa a Malawi kudabwa kuti chomwe chinavuta a Msungama ndi chani kwenikweni. Anthu ena ayambapo kunena kuti a Msungama anapita mu dziko la India kuti akabise Danzi lawo limene layamba kuonekela mowala.

Koma a Msungama eni ati iwo anapita mu dziko la Inida ndi vuto la mwendo ndipo ali kumeneko anapezelapo mwayi oti achita opeleshoni yobwenzeletsa tsitsi mmutu.

Malinga ndi malipoti a atolankhani, a Msungama ati anawauza kuti boma silinalipile dongosolo lothana ndi Danzi lawo ndipo mmalo mwake lalipila ndi bungwe lothandiza anthu pa za umoyo wawo la MASM.

“Boma langolipila za chithandizo cha mwendo wanga, zakuthana ndi danzi langa alipila ndi a bungwe la MASM,” akuti a Msungama anatelo.

Koma anthu odziwa momwe bungwe la MASM limagwilila ntchito ati ndi kosatheka kuti bungweli likalipile ndondomeko yobwenzeletsa tsitsi kapena kuti yochilitsa munthu ku matenda a Danzi.