Mboro wadya Bushiri mu round yoyamba

Advertisement

Mtumiki wotchuka kwambiri muno mu Africa, Shepherd Bushiri, sizinawathere bwino ku South Africa komwe akudzulidwa ndikudyedwa ndi Bambo Mboro. Iwo agonjetsedwa mu round yoyambayeniyeni pakukumana kwaoku.

Mwakuti pano anthu akuti Mboro watsiya Bambo Bushiri alitapsa kwinaku akudikira kuti alowe round yachiwiri.

A Bushiriwa anasumila mtumiki mzawao Paseka Motsoeneng omwe owanyadira amawatcha kuti Bambo Mboro.

Bushiri wagonja kwa Mboro

A Bushiri akufuna chindaputsa chokwana pafupifupi 50 million Kwacha kufumira kwa a Baba Mboro chifukwa chowaipitsira a Bushiriwa dzina.

Koma podikira chilamulo chamulandu wa “Undinyozeranji Iwe Mboro”, a Bushiri omwe akhala akudyera limodzi ndi a Mboro m’mbuyomu anakamang’alanso ku bwalo lamilandu la South Africa.

Iwo akuti anapempha a Bwalo kuti liwatseke pachigama a Mboro kuti asiye kusiya kamwa. Koma a khoti anati mulanduwu ngwa washiawuti ndipo anati sakuonapo chifukwa choti a Mboro n’kuletsedwa muzichitochito za malankhulidwe awo.

Mwakuti tikukamba pano, Mboro yamugonjetsa Bushiri mukukumana kwawo koyamba.

Angakhale a Bushiri adyedwa ndikukudzulidwa ndi Mboro nasiyidwa akupumira m’mwamba a Major 1, mlandu oyipitsirana dzina uja ukupitilirabe ndipo ife tikudziwitsani momwe umo dzithere pakukumana kwawo kwachikena.

Zonsenzi zikuchitikira mu bwalo la Milandu la likulu ku South Africa.

Advertisement