Nkhondo pachiweniweni: Aphungu a DPP atengelana ku khothi

Advertisement

Phungu wa chipani chotsutsa boma cha DPP kum’mwera m’boma la Thyolo a Chimwemwe Chipungu atengera ku khothi phungu nzawo wa DPP m’boma la Blantyre a Noel Lipipa.

A Chipungu ati akasumila a Lipipa kaamba kowaipitsira mbiri kuti iwo adaba ndalama zomwe mtsogoleri wakale wadziko lino yemweso ndi mtsogoleri wa DPP, a Peter Mutharika, anapeleka kuchipanichi.

Malingana ndi chikalata chakukhothi chomwe Malawi24 yaona, a Lipipa atengeledwa ku khothi kaamba koipitsira mbiri phungu mzawoyo pandalama zomwe akuti a Mutharika anapeleka ku chipanichi.

Chipungu

Nkhaniyi ikusonyeza kuti nthawi ya kampeni pazisankho zapitazi a Mutharika omwe ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP anapeleka ndalama kuchipanichi kuti zigwiritsidwe ntchito pokopera anthu.

Koma malingana ndi a Lipipa, a Chipungu anadya ndalamazi zomwe a Mutharika anapelekazi.

A Lipipa akuti anaulutsa za nkhaniyi pomwe analemba zankhaniyi pa gulu la WhatsApp yomwe pali anthu 156.

Ngakhale zili choncho, a Chipungu akanitsitsa mwantu wagalu kuti iwo sanadye ndalamazi ndipo ati akufuna kuti a Lipipa awapepese ndi ndalama kaamba kowaipitsira mbiri ndi nkhaniyi yomwe ati ndiyabodza.

Pakadali pano a Lipipa auzidwa kuti akozekere kupititsa mboni za nkhaniyi pomwe posachedwapa akuyembekezeka kukaonekera kukhothi.

Advertisement