MEC yapempha kudekha, bata panthawi yachisankho

Advertisement

…50+1 ndiyomwe igwiritsidwe ntchito….

Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lapempha anthu kuti akhale odekha komanso asunge bata ndi mtendere pomwe dziko lino likhale likuchita chisankho cha mtsogoleri wadziko lachiwiri lino.

Izi ndimalingana ndi wapampando wa bungwe la MEC a Chifundo Kachale omwe amayankhula pa msonkhano wa atolankhani lamulungu mu mzinda wa Blantyre.

Mwa zina a Kachale anati bungweli lakonzeka bwino kupangitsa chisankhochi ndipo chilichonse chili m’malo mwake ngakhale kuti ati akupeleweledwa ndalama yokwana MK10 billion yoti alipilire zinthu zina zomwe agula zachisankhochi.

Iwo anatiso zipani zonse zili ndiufulu oti zitha kutumuza nthumwi zake kuti zikakhale nawo pamwambo owonetsetsa kuti katundu yese wachisankho wafika ndipo palibe chovuta chilichose.

Mkuluyu walangiza anthu kuti akhale odekha komaso asunge bata ndi mtendere panthawiyi ponena kuti phuma komaso mapokoso amabweletsa ziwawa zomwe zimasokoneza mtendere wa dziko lathu lino.

Apa a Kachale anati ngati njira imodzi yolimbikitsa bata komaso mtendere panthawiyi, bungwe la MEC liwonetsetsa kuti madandaulo onse omwe angatuluke panthawiyi azathane nawo mumasiku ake oyikika.

“Ife a MEC tikufuna tipemphe mobwereza kuti chonde aMalawi tikhale odekha, chonde aMalawi tikhale osunga bata kuti masankhowa akhale a mtendere ndipo aliyense amene adzaluze adzavomeleze kuti chilungamo chachitika.

“Ndichifukwa chake tikufuna kudzudzula anthu aliwonse amene angafune kuletsa, kuopsyeza kapena kulepheletsa anzawo omwe angafune kukavotera malinga nchomwe iwowo akufuna kuti opezeka akuchita izi lamulo lidzagwira ntchito, ” anatero Kachale.

Poyankha funso loti ngati bungweli lingagwiritse ntchito njira yoti munthu owina akuyenera kupeza ma voti oposela 50 pelesenti kapena ayi, wapampandoyu anati bungweli ligwiritsa ntchito zimene linanena khothi zoti MEC igwiritse ntchito ndondomeko ya 50+1.

Apa a Kachale anati chomwe anthu akuyenera kudziwa kwambiri nchoti bungweli likuyendetsa chisankhochi mogwirizana ndizomwe bwalo la milandu linagamula ndipo anati awonetsetsa kuti chilichose chomwe khothi linanena chitsatidwe.

Pakadali pano, MEC yatsutsa mphekesera yoti kwapezeka katundu wachisankho ogwiritsidwa kale ntchito zomwe ati ndibodza la mkunkhuniza koma avomereza kuti katundu yemwe anasowa ku Dedza wapezeka koma sanagwiritsidwe ntchito, ali momwe analili.

“Tikufuna titsutse mphekesera zomwe zakhala zikumveka kuti kwina kwapezeka ma pepala ovotela ochonga kale ili ndibodza ndipo palibe komwe izi zachitika,” anaonjezera choncho a Kachale

Advertisement