Adad ayenda choduduluza ngati yakwa Manje


Mwakhala mukuona momwe ayendera magalimoto akwa Manje kapena malore otuta njerwa ndi mchenga omwe sitati yake imakhala yoduduluza buleki n’chikang’a.

Umu ndi momwe anayendera a Pulofesa a Peter Mutharika omwe owanyadira amati adad popanga kampeni.

Vidiyo yomwe ikugawidwa kwambiri pa masamba a mchezo ikuonetsa apolisi akukankha galimoto ya bode yomwe a Mutharika anakwera.

Pamenepa nkuti a Mutharikawo atangokhala pa mpando ku bodeko paulendo wawo ocheza ndi anthu dzulo.

Paulondewu, a Mutharika anachoka ku nyumba ya Sanjika ku Blantyre kuima pa Lunzu, pa Ntcheu boma komanso pa Biwi mu mzinda wa Lilongwe.

Polankhula ndi anthu kwa Biwi, a Mutharika anapempha a Malawi kuti azawavotere pa chisankho cha pa 23 June ndipo iwo adzaonetsetsa kuti Malawi atukukuke ndikumaoneka ngati dziko la Amerika.

Mawa a Mutharika akhala akuchoka ku Lilongwe kukapangaso kampeni ku Kasungu, ku Mzimba ndi ku Mzuzu.