Gwamba wayela ngati matalala: ena akuti ngati Vybz Kartel

Advertisement

Katswiri oyimba nyimbo za uzimu za chamba cha hip hop Duncan Gwamba Zgambo wadabwitsa anthu pamene wayela khungu poyelayela.

Gwamba amene amakhala mu dziko la South Africa waoneka mwatsopano kudzera pa chithunzi chake chomwe anaika pamasamba a mchezo, masiku awiri apitawo. Izi zadabwitsa anthu popeza mnyamata yu sanaonekepo oyera khungu.

Othilira ndemanga nawo posafuna kuphweketsa ati nkutheka katswiriyu akumagwiritsa ntchito mafuta oyeresa khungu. Enanso ati itha kukhaka mphamvu ya phone ya mmanja yomwe adagwiritsa ntchito pozijambula.

Aka sikoyamba kuti anthu athilire ndemanga pa nkhani yokhudza Gwamba. Chaka chapitacho, nkhani yokhudzana ndi kuchepa thupi kwake inali mkamwamkamwa kwathu kuno.

Olankhula anati Duncan wachepa thupi chifukwa amachita masewera olimbitsa thupi. Otsutsa nawo posafuna kungokhala adati oyimba yu adachepa thupi kamba ka matenda.

Aneni ena anena, Gwamba Duncan Gzambo, akuoneka ngati katswiri wa ku Jamaica Vybz Kartel amene anagwiritsa ntchito njira zamakono zowezukitsa khungu.

Advertisement