Joyce Banda anandikwiyila chifukwa ndinamuletsa kupititsa ‘uhule wake wa ku Lilongwe ku China – APM

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wayambapo kumema anthu kuti azamuvotele pa chisankho chimene chikuyenela kuchitika chaka chino ndi moto ndi ukali.

Pa msonkhano ongoima umene anachita ataima kwawo kwa Goliati pochokela ku sukulu ya ukachenjede ya MUST, Mutharika anayankhula monyodola kuyankha a ndale amene anamulalatila pa Njamba sabata latha.

“Joyce Banda akunena kuti ine ndimamwa kachaso, ine sindimwa kachaso, ndi zabodza,” anatelo a Mutharika kuuza anthu amene anasonkhana.

“Ndikuuzani kumene nkhani inayambila, kunali ku China,” anatelo a Mutharika.

A Mutharika ndi mayi Mutharika pansonkhanowo

A Mutharika anati Mayi Banda ankafuna kutenga chipinda choyandikana ndi amene anali mtsogoleri wa dziko pa nthawi imeneyo a Bingu wa Mutharika.

“Ine ndinawakaniza ndipo udani wathu unayambila pamenepo,” anatelo a Mutharika.

Iwo anaonjezela kuti Mayi Banda anakwiya chifukwa chokanizidwa kugona chipinda choyandikana ndi mtsogoleri wa dziko.

“Ine ndinati iyayi, sindilola kuti uhule wako wa ku Lilongwe ubwele nawo kuno,” anatelo a Mutharika.

Pa msonkhano wa ku Njamba, Mayi Banda ananyoza a Mutharikla kuti iwo ndi okonda kachaso.

“Ine sindimwa kachaso, ndimamwa wine pan’gono,” analongosola a Mutharika.

Advertisement