Boma liyamba kuthandiza ovutikitsitsa m’mizinda

Advertisement
Malawi24.com

Ngati njira imodzi yochepetsera chiopsezo chanjala yadzaoneni makamaka kaamba kanthenda ya COVID-19, boma la Malawi lalengeza kuti liyamba kupereka thandizo kwa mabanja ovutikitsitsa m’mizinda yose yadziko lino.

Izi ndimalingana ndichikalata chomwe boma latulutsa lamulungu pa 19 April chomwe chati ndondomekoyi iyamba posachedwapa kumizinda yonse yomwe ndi Blantyre, Mzuzu komaso Lilongwe.

Malingana ndi chikalatachi, cholinga chenicheni cha ndondomekoyi ndi kuthandiza mabanja ovutikitsitsa omwe amadalira ndalama yopeza tsiku ndi tsiku kuti athandizike pa moyo wao munyengoyi pomwe dziko lino lakhudzidwa ndi mlili wa COVID-19.

Boma lati pakadali pano makhonsolo akhala akuchita kaundula oyenera m’mizindayi m’madera okhaokha m’mene mumakhala anthu ochepekedwawa ndipo latsindika kuti ndi anthu ovutikitsitsa okha amene adzalowe mu kaundulayi.

Chikalatachi chatiso kaundula wa anthu ovutikitsitsayu ayamba masiku akubwerawa pogwiritsa ntchito achinyamata omwe azidzayenda m’makomo motsatira mdandanda wa m’makomo (household list) omwe ma khonsolo ndi Madera ali nawo kale.

“Boma La Malawi likudziwitsa anthu onse kuti malingana ndi mliri wa corona omwe wakhuzanso dziko la Malawi, Boma kudzera m’ma khonsolo am’mizinda ikulu-ikulu ndi thandizo lochokera ku boma komanso kumabungwe osiyanasiyana lakonza ndondomeko zofuna kuthandizira mabanja ovutikitsitsa amene akupezeka mmizinda,” latelo boma.

Chikalatachi chatiso anthu aku khonsolo adzalemba mndandanda wa mayina a makomo ndi manambala a lamya zawo ndi malo omwe anavomerezeka kuti anthu ovutikawo amachokera.

Ilo latiso anthu osankhidwa mu ndondomekoyi, adzidzalandira thandizoli kudzera mu njira za makono pa lamya kapena ku
banki.

Boma likudziwitsaso anthu onse kuti pamene ntchito yothandiza anthu ovutikitsitsa m’mizinda ikulu-ikulu ikukhazikitsidwa, pologalamu ya ‘Mtukula pa Khomo’ ikhala ikupitilirabe m’maboma onse a mdziko lino.

Advertisement