Bambo aotcha nyumba ya mkazi wake wakale

Advertisement
Malawi24.com

Bambo wa zaka 35 wochokela m’mudzi mwa Tsadoka, mfumu yaikulu Malemia ku Nsanje waotcha nyumba ya mkazi wake wa kale ku Nsanje komweko atamukaniza kutenga ana.

Otsatira wa mneneli wa polisi ku Nsanje a Pilirani Kondwani avomeleza kuti nkhaniyi ndiyowona ndipo apolisi m’bomalo akusakasaka bambo Macdonald Thomasi omwe adandaulidwa kuti aotcha nyumba ya mayi Peterson.

Odandaula, a Mary Peterson, anauza a polisi ku Nsanje kuti amuna awo akale, bambo McDonald Thomas aotcha nyumba atawakaniza kutenga ana awo.

Mayiwa anati banja lawo ndi bambo waotcha nyumbayi linatha mu chaka cha 2019 ndipo anawasiya ali ndi ana awiri.

Patadutsa nthawi bamboyi osaonekela komanso kupeleka chithandizo cha mtundu wina ulionse kwa ana ake chitheleni banja, bamboyi anabwelela kwa mkazi wake wakaleyu dzana pa 28 February kuti akatenge ana ake.

“Ndipo mayi Peterson anakanitsita kupeleka anawo. Izi zinakwiyitsa bambo Macdonald mpaka anayatsa nyumba zomwe zinapangitsa kuti katundu yense wa mnyumba yomwe inaotchedwayo awonongeke,” anatero a Kondwani.

Advertisement