ECM, NICE ipempha bata ndi mtendere

Advertisement

Pamene kwatsala masiku ochepa kuti bwalo lamilandu lipeleke chigamulo pa mlandu wachisankho, bungwe la chikatolika la ECM komaso bungwe lophunzitsa anthu pazinthu zosiyanasiyana la NICE apempha anthu mdziko muno kuti asunge bata ndi mtendere.

Izi ndi malingana ndichikalata chomwe mabungwe a Evangelical Conference of Malawi atulutsa lamulungu pa 26 January mogwirizana ndi bungwe la National Initiative for Civic Education.

Mu chikalatachi chomwe Malawi24 yawona, mabungwe awiriwa atsindika mwachimvemve kuti zinthu sizili bwino m’dziko muno ndipo apeleka chitsanzo chakugawanika kwa anthu kaamba ka mpungwe pungwe pa ndale.

ECM ndi NICE ati ndi zodandaulitsa kuti anthu ambiri mdziko muno sakumwerana madzi kaamba ka ndale zomwe zabweretsa chipwilikiti ndi ziwawa zosatha ndipo ati anthu iwala kuti Mulungu anadalitsa dziko lino ndi bata komaso mtendere.

Mamulumuzana awiriwa atiso chodandaulitsa china ndi choti Mulungu anapeleka mwai kwa anthu mdziko muno osankha tsogolo lawo koma m’malo mwake ambiri asankha imfa osati moyo pokonda zionetsero zomwe ati zathandizira kuononga zinthu mdziko muno.

“Monga tidafotokozanso m’mbuyomu, tikayang’ana m’mene zinthu zilili m’dziko lathu lino masiku ano, tingathe kunena motsimikiza kuti Amalawi tili pampungwepungwe ndipo tikapanda kusamala ndikuchitapo kanthu, zinthu zitha kusokonezeka mosakomera tonsefe.

“Zimene Mpingo Wakatolika mogwirizana ndi Bungwe la NICE likufuna kuti ife tonse tichite ndikuganizira mozama ndizakuti palibe amene angakonze tsogolo ladziko lathu lino kupatula ife eni ake Amalawi’.” Latero gawo lina la chikalatachi

Mabungwewa auzaso atsogoleri andale kuti ndi omwe akuenera kukhala patsogolo kulimbikitsa bata ndi mtendere ponena kuti anthu amatengera zomwe atsogoleri awo akupanga kapena kuwauza kuti apange.

Apa ECM ndi NICE yapempha azitsogoleri azipani kuti awuze otsatila awo kuti asunge bata bwalo lamilandu likatulutsa chigamulo chake ndipo otsatira zipani awauzaso kuti asalore atsogoleri awo akawalimbikitsa kuphwanya ufulu wa ena.

“Tisalore atsogoleri kutilimbikitsa kuti tiphwanye maufulu a anthu ena powamenya, kuchitaziwawa, kuphwanya zinthu ndipo tidziwe kuti kuchita izi ndimilandu yaikulu,” yatero ECM ndi NICE.

Mabungwewa ati anthu adzifuse kuti nchifukwa chiyani andale samalora ana awo kutenga nawo gawo pa zionetsero zomwe anazitchula kuti zimakhala zaupanda ndipo zimabweretsa chiwawa mdziko muno.

ECM ndi NICE yatsendera ndikuwakumbutsa anthu kuti pamlandu uli onse pamakhala mbali imodzi yomwe imapambana ndipo ati anthu ayembekezeso kuti zotsatira zamlanduwu zikomera mbali imodzi koma ati ndikofunika kuti anthu avomeleze zotsatirazo komaso asunge bata.

Bwalo la milandu likuyenera kupeleka chigamulo chake pa mlandu wachisankho sabata ino kapena kumayambiliro kwa sabata yamawa.

 

Advertisement