UTM yazitaya pa chisankho chapadera

Advertisement

Chipani chotsutsa boma cha UTM chomwe mtsogoleri wake ndi a Saulos Chilima, chalengeza kuti sichipikisana nawo pa chisankho chapadera ku Lilongwe ndi ku Kasungu.

Izi ndimalingana ndi m’neneri wa chipanichi a Joseph Chidanti Malunga omwe atsimikiza za nkhaniyi.

Malaunga: Sitipikisana nawo

A Chidanti Malunga ati chipani cha UTM chapanga ganizo losapikisana nawoli kaamba koti chataya chikhulupiliro ndi bungwe loyendetsa zisankho la MEC lomwe ati silinayendetse bwino chisankho chapitachi.

Iwo ati bungwe la MEC silikuyenera kuyendetsa chisankho chilichose chifukwa linalephera kuyendetsa chisankho cha patatu pa 21 May chaka chino.

Poonjezera pa izi, mneneri wa UTM yu anati akuona kuti zikhala zinthu zopanda nzeru kuti chipani chawo chitenge gawo pachisankho cha mwezi wa mawachi kaamba kuti chipani chawo chikutsutsana ndizotsatira za chisankho cha mu May ndipo nkhani yake ili ku khothi.

Izi zikubwera pomwe chipanichi posachedwapa chinabwera poyera ndikuika a Samson Phinifolo kuti ndiomwe apikisane nawo pachisankho cha phungu ku m’mwera kwa mzinda wa Lilongwe kutsatila imfa ya a Agness Penemulungu omwe aanamwalira patatsala masiku ochepa kuti chisankho chichitike.

Pakadali pano chipani cha MCP chomweso chikutsutsa zotsatira za chisankho cha pa 21 May, chati chitenga nawo gawo pachisankho cha chibwerezachi m’madera onse awiri ngakhale kuti chili ndi mkwiyo ndi bungwe la MEC.

Posachedwapa, Bungwe la MEC linati zonse zili mchimake kuti lipangitse chisankhochi pa 5 mwezi wa mawa ndipo la chitatu pa 16 October bungweli limalandira zikalata kwa anthu amene akuyenera kupikisana nawo pachisankhochi

Advertisement