Tay Grin alonjeza sukulu ya u dalaivala yaulere


Katswiri oyimba nyimbo zachinyamata ameneso akuimira uphungu wa nyumba ya malamulo ku Lilongwe City Centre Constituency Tay Grin wapanga lonjezano lakuya pamene zisankho zikuyandikira.

Tay Grin amene dzina lake lobadwira lili Limbani Kalilani, walonjeza kuti wachinyamata aliyese mudera lomwe akuimira, alandira maphunziro aulere a kayendesedwe ka galimoto.

Tay Grin: ayambisa sukulu ya udalaivala

Izi zatsimikizidwa pa tsamba la mchezo la Facebook la bambo Kalilani. Iwowa anenetsa kuti wachinyamata aliyese amene adalembesa mu kaundula wa mavoti, mu dera lomwe akuimira, akhala ndi mwayi ophunzira kuyendesa galimoto mwaulere.

Iyi ndi imodzi mwa njira zomwe Limbani akufuna agwiritse ntchito kuti anthu azamusankhe pa chisankho cha patatu chomwe chizachitike mu Mwezi wa May.

Anthu ena athilirapo ndemanga pofunsa kuti katswiriyu adali kuti nthawi yonseyi m’mene achinyamata amkasowa mwayi wa nzama opalasa ndi manja Khasu lilipo, ngati umeneyu?

Koma potengera kuti ino ndi nyengo yomwe andale akukopa anthu kuti azawasankhe, ena sakuona cholakwika ndi ndondomeko yomwe woyimbayu akufuna kukhadzikitsa.

Grin akuyimira chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP). Iyeyu, wasata Mai ake, Dr Jean Kalilani amene ali phungu wa chipani cholamulanchi mu boma la Dowa komaso nduna ya boma.