Tchimo langa ndikukhala mpondamatiki wa ku Malawi, watero Bushiri


Prophet Shepherd Bushiri Major One

M’modzi mwa aneneri otchuka mdziko muno yemwe anamanga maziko ake ku South Africa, mneneri Shepard Bushiri wati tchimo lomwe limamupangitsa kukhala oyipa m’dziko muno ndi kukhupuka.

Mneneri Bushiri wati anthu ochuluka Ku Malawi kuno amamuda kamba koti ndim’modzi mwa anthu omwe akuchita bwino pankhani za malonda ndipo wanenesa kuti tchimo lake ndiloti ali ndichuma chankhaninkhani.

Iye amayankhula izi mumzinda wa Blantyre pomwe amakhazikitsa mabuku omwe walemba ndipo atulutsidwa posachedwapa.

“Anthu Ku Malawi kuno samakondwa akakuona ukupita chitsogolo. Amakondwa akakuona ukulephera. Ngati mukuona kuti ndikunama muike sitetasi yokhumudwa pa fesibuku kapena watsiapu, ndipo pakatha ola muikeso sitetasi Ina yoti; Mulungu wandipangira, khulupilirani anthu ambiri ayankha zankhani yanu yokhumudwayo,” watelo mneneri Bushiri.

Iye anaonjezera kuti nthawi zonse mMalawi akalemera anthu amamunena kuti wayamba ufiti kapena wayamba sataniki ndipo anati zimene anthu amamuganizira zoti analowa sataniki ndizabodza.

Fisi anakana msatsi; Bushiri wati chuma chomwe ali nacho ndichifukwa cha thukuta lomwe amakhetsa pa malonda osiyanasiyana omwe amapanga ndipo watemetsa nkhwangwa pamwala kuti iye siwasataniki.

“Ndakhala ndikutonzedwa kwambiri ndi anthu oipa omwe amandinena kuti ineyo ndakhala ndikupangitsa ngozi zapansewu. Ndimathandiza anthu ochuluka koma palibe amene amayankhula kanthu. Choipa chikangochitika kwa mmodzi mwa anthu zikwizikwi omwe ndimathandiza, ndimaikidwa pamtanda ndipo ndimatchedwa wa sataniki,” analira chokweza mneneri Bushiri.

Munthu wa Mulunguyu anapitiliza kulira kwake ndimau oti nthawi zambiri amadandaula amasweka mtima kaamba koti anthu mdziko muno samasangala kuona mmodzi mwa mzika zimzawo zikutukuka.

Ngakhale wati iye chuma chake chochulukacho samafuna kuti chikhale mdziko lino, mneneriyu wati sasiyabe kuthandiza ndipo wati ali ndimalingaliro oti azithandiza ndi ndalama zochuluka imodzi mwa ma banki dziko lino..

Bushiri anapitilira ndikuthokoza mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika kaamba kokonza nsewu wamakono mumzinda wa Mzuzu komaso nsewu wa Mzuzu-Nkhatabay.

Ena mwa mabuku omwe mneneriyu amakhazikitsa ndimonga; Names of God, Mysteries Surrounding Your Money, Crafts for Effective Public Speaking and Sleeping Near the Ark.

Ena mwa anthu omwe anafika pa mkumanowu ndi akuluakulu aboma, monga wachiwiri kwa nduna ya za mmdziko ndi chitetezo a Charles Mchacha, andale monga Brown Mpinganjira, Dr Ben Phiri, mlakatuli Hudson Chamasowa, Paramount Chief Kaomba, komaso Dr Pearson Nkhoma.

One comment on “Tchimo langa ndikukhala mpondamatiki wa ku Malawi, watero Bushiri

Comments are closed.