Yalakwa! mafuta akweranso mtengo, ma minibus nawo ali m’mbuyomu


Mzuzu

Patangodutsa masiku owerengeka chabe boma la Malawi litakweza mitengo ya mafuta a galimoto, mitengoyi yakwezedwaso.

Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe chatulutsidwa lachitatu ndi bungwe loyang’anira mafuta m’dziko muno la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA).

Mzuzu
Mtengo wa mafuta wakweraso

Malingana ndi akulu akulu a MERA, chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga ndi kukwera kwa mafutawa pamsika wa mafuta pa dziko lonse la pansi komaso kugwa mphamvu kwa ndalama yathu mdziko muno.

Iwowo ati izi zawakakamiza kukweza mafuta a petrol kuchoka pa MK932.50 kufika pa MK990.30, mafuta a diesel achoka pa MK935.60 kufika pa MK990.40 ndipo mafuta a parafini afika pa MK785.0 kuchoka pa MK755. 30.

Anthu ena m’dziko muno sanailandile bwino nkhaniyi ndipo ena akulitonza boma kuti silimasalira miyoyo ya anthu mdziko muno.

M’modzi mwa anthu oyankhula pa nkhani zonga izi, a Onjezani Kenani ati chifukwa chomwe boma lapeleka pa zakukwera kwa mafutaku ndi bodza la mkunkhuniza.

Iwo ati lachiwiri sabata ino mafuta pa msika wa dziko lonse anatsitsidwa ndi 7 peresenti zinthu zomwe ndizosiyana ndizomwe boma lanena.

“Padziko lonse la pansi, mafuta anatsitsidwa mitengo ndi 7 percent lachiwiri lapitali koma kwathu kuno ku Malawi akweza ndi 6 percent patangotha masiku awiri okha.” watero Kenani.

Pali chiopsezo choti mitengo ya zinthu zochuluka kuphatikizapo mitengo ya mayendedwe ikwera potsatira kukwera kwa mafutawa.