Kadaulo pankhani yoyimba nyimbo za uzimu mu chamba cha hip hop Gwamba wanenesa kuti ayimbira Namalenga mpaka kusasa mawu.
Gwamba watero mu maimbidwe ake atsopano otchedwa Kusasa Mawu. Nyimboyi yomwe yajambulidwa masabata ochepa apitawo, ikukondedwa ndi a Malawi ambiri.
“Ndiimbira Yehova mpaka kusasa mau ine, wandipasa kagelo,” ayimba motero namanyonyoloyu.
Maimbidwe amenewa ndi otamanda Mulungu, makamaka pompatsa njole yaku mtima kwake. Katswiri yu waphatikiza zachikondi ndi za uzimu mu nyimboyi zomwe zikusonyeza luso lake pa mayimbidwe.
Kukamba za majambulidwe a nyimboyi, ndiogomesa osati masewera. Zing’wenyeng’wenye zodzetsa mudyo zilimo ndithu. Ngakhale Gwamba amaimba mu chamba cha hip hop, mu nyimboyi waimba mwa timawu ta nthetemya mogwirizana ndi zida.
Uthenga ukumveka ndithu mochitira umboni zoti Gwamba adafatsa polemba nyimbo imeneyi yomwe yamusasisa mau.
Pofuna kukometsa zinthu, oyimba yu adajambulanso kanema wa Kusasa Mau mwa luso. Mawayilesi a kanema mu dziko lino agoma nazo ntchito za bamboyu.