Maluzi atiswa – yatelo PP

Advertisement
pp

Ehede! Mwawakumbukila aja ankalandira za Lutepo aja uku akuzitukumula. Aja anali ndi galimoto kholophethe ali mu boma aja. Tsopano akuti maluzi awasasantha.

Mneneri wa chipani cha PP a Noah Chimpeni wati chipanichi chilibe ndalama zoti ndikuyitanitsila msonkhano waukulu osankha oyimila chipanichi pa masankho a 2019 ndi akulu akulu ena a mu chipani.

Noah Chimpeni-PP
Chimpeni: Chipani cha PP chilibe ndalama zoti ndikuyitanitsila msonkhano waukulu

A Chimpeni ati ndi mmene zinthu ziliri, sangathenso kunena kuti apanga liti msonkhano waukuluwu kamba koti anthu akufuna kwabwino sakuoneka oti mwina ndikuwathandiza. Koma iwo ati anthu asataye mtima chifukwa msonkhano umenewu uchitikabe.

Iwo aonjezelapo kuti padakali pano zikuoneka kuti anthu onse akufuna amayi Joyce Banda aimile chipanichi pa 2019.

Advertisement