Abwelako chabe: anyamata a Chilima akumana ndi mbonaona ku nyumba ya malamulo

Advertisement
Saulos Chilima

Akanakhala a Saulos Chilima kuti akuthilira ndemanga pa nkhaniyi mwina akanati andione andione anakhalira zinthu zake zomwe; kapena akanati n’konze n’konze ananyula a weni maliro?

Aphungu amene ali patsogolo poyendetsa ntchito ya a Chilima kuti atenge u President dzulo atuluka mu nyumbayi nkhope zili zyoli atalephera kupita patsogolo ndi nkhani yawo yofuna kuletsa anthu odutsa zaka 65 kuyimila pa udindo.

Bon Kalindo
A kalindo ali patsogolo poyendetsa ntchito ya a Chilima kuti atenge u President.

Anayambitsa nkhaniyi ndi a Chidanti Malunga ndipo inatsatizidwa ndi a Bon Kalindo. Iwo ati amafuna kusintha malamulo kuti anthu onse okwanitsa zaka 65 asamaloledwe kuyima pa mpando wa President.

Koma pothilapo ndemanga pa nkhaniyi, a Peter Dimba a Kongeresi anadzudzula mwamphamvu awiriwa kuti asiye u madyelamphoto ofuna kuthanilana ndi nkhani zachipani mu nyumba ya malamulo.

“Osagwilitsa nyumba ya malamulo ngati chikwapu chanu chothibulilana mu chipani. Sitingamapange malamulo kuti tithane ndi munthu ayi,” anatelo a Dimba.

Iwo anaonjezelapo zitsanzo za a Kamuzu Banda ndi a Bingu wa Mutharika amene apanga zinthu mu dziko muno koma adali oti adutsa zaka 65 zimakambidwazo.

Atamaliza a Dimba, nyumba ya malamulo inawaombela m’manja modabwitsa zimene zinaopsa a Malunga ndipo iwo anakana kupitiliza nkhaniyo ndi cholinga choti Aphungu avote.

Ndipo phungu wina amene amati akayamba nkhani yoti president aziyimbidwa milandu ali pampando sanabwele ndi komwe ku nyumba ya malamulo.

Advertisement

5 Comments

  1. Aaaaa Mr bon kalindo nd azanu mukupupuluma bwanji? Mupusa nazo izi…..

  2. Kamuzu Banda & Bingu wa Mutharika osamaphatikitsa ndi Peter wa Mutharika, Peter wakaramba mupusa

  3. Asagwilitse nchito nyumba ya malamulo Nkhani zachipani ayi zimenezo akambilane ku chipani komweko

Comments are closed.