Konzekani, kukubwela Mvula yoononga kuyamba lachinayi

Advertisement
Storm

Kodi mwaona kale kuti nyumba zanu ndi zodalilika? Ndiye kuli zimbudzi, zija zimangogwa ndi Mvula, munamanga zolimba?

Bungwe loona za nyengo mu dziko muno lanena kuti a Malawi akhale okonzeka chifukwa Mvula ya mphamvu ikuyembekezeleka kukhuthuka m’dziko muno kuyambila mawa lachinayi.

Joram Nkhokwe: a Malawi akuyenera kukhala okonzeka.

Malinga ndi wamkulu wa bungweli ndi katswiri oona za nyengo a Joram Nkhokwe, mphepo ya ku Congo ndiyo igwetse Mvula yoopsayi ku Malawi.

A Nkhokwe ati madera ngati a ku Lower Shire, Dedza ndi ena ku Karonga ali pa chiopsezo choti madzi atha kusefukila kamba ka mvulayi.

A Nkhokwe ati anthu madera a kumeneku akungoyenela kukhala okonzeka olo kusamuka kumene kamba ka Mvula imeneyi yomwe itha kuika moyo ndi katundu wawo pa chiopsezo.

Mvulayi ati ikuyembekezeleka kukhuthuka kuyamba mawa lachinayi kufika lamulungu ndipo pena izibwela ndi mabingu.

 

Advertisement

11 Comments

  1. KApe iweso nkhani imeneyi?akapo zoti tidziwerenga zazeru wanva like izi akuchita amuthalika ndi boma lawo kuti amalawi azidziwa ulesi bwanji mkulu ?

  2. kkkkkkkk telling us what he is thinking….not what God will do for us….

Comments are closed.