Nkhanza za Chakwera zandipititsa ku DPP – Jumbe

172

Wazitaya. Wazinyanyala. Wazidomoka. Wayendela yake. Wapita atanyangala ndipo walalika kuti a Chakwera ndi munthu wa nkhanza asananyamuke.

Phungu wa dera lapakati mu boma la Salima a Felix Jumbe alengeza kuti tsopano alowa chipani cholamula cha DPP.

Felix-Jumbe

a Jumbe alowa chipani cha DPP

A Jumbe alengeza izi kudzela pa tsamba lawo la Facebook kuti tsopano iwo ndi a chipani cholamula ndipo mu 2019, iwo akuima ngati wa DPP.

A Jumbe anenanso kuti iwo sazaimanso ku dera lawo lapano, ati m’malo mwake akukayima ku dera la kumpoto mu boma la Salima lomwelo komwe kuli kwa Mayi awo.

Atauzidwa kuti iwo akagonja kumene akupitako kamba koti DPP ilibe chikoka, a Jumbe adanena kuti anthu ndiwo awatuma.

A Jumbe adachotsedwa mu chipani cha Kongeresi mu chaka cha 2016.

Ngakhale adatenga chiletso ku bwalo la milandu, a Jumbe ndi Kongeresi akhalila kulumana.

 

Share.
  • Opinion